Pitani ku nkhani yake

SINGAPORE

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Boma la Singapore limakakamiza anthu kulowa usilikali ndipo silipereka ufulu wokana usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira. Achinyamata a Mboni za Yehova omwe akana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, amalamulidwa kuti akakhale m’ndende maulendo awiri otsatizana ndipo amakhala m’ndendemo kwa miyezi 39.

Ku Singapore, mnyamata akakwanitsa zaka 18 amayenera kulowa usilikali. Ngati angakane chifukwa cha zimene amakhulupirira, amasungidwa mukampu ya asilikali kwa miyezi 15. Miyeziyi ikatha, amatulutsidwa ndipo kenako amalamulidwa kuti avale yunifolomu ya asilikali kuti ayambe kuphunzitsidwa ntchito yausilikali. Akakananso kuchita zimenezi, amazengedwa mlandu kachiwiri ku khoti la asilikali ndipo amatha kulamulidwa kuti akhale mukampu ya asilikali kwa miyezi 24.

Dziko la Singapore Likukana Kutsatira Zomwe Bungwe la UN Linanena

Kwa nthawi yayitali, bungwe la United Nations lakhala likuuza mayiko onse omwe ndi mamembala ake kuti “aziona kuti kukana usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira n’kogwirizana ndi ufulu woganiza, wochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima, komanso ufulu wokhala m’chipembedzo malinga ndi zimene zili mu chikalata cha mfundo za ufulu wa anthu (Universal Declaration of Human Rights).” Ngakhale kuti dziko la Singapore lakhala lili membala wa bungwe la United Nations kuyambira mu 1965, dzikoli lasonyeza kuti silikufuna kutsatira zimene bungweli linanena pa nkhaniyi. M’kalata yomwe mmodzi wa akuluakulu a boma la Singapore analembera bungwe la UN Commission on Human Rights pa 24 April, 2002, ananena kuti “ngati zimene munthu amakhulupirira kapena zochita zake zikutsutsana ndi ufulu woteteza dziko womwe boma lili nawo, ufulu wa boma ndi umene uyenera kutsatidwa.” Iye analembanso motsindika m’kalatayo kuti: “Tikuona kuti m’dziko lathu sitingatsatire zimene mayiko ena amachita polola anthu kukana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.”

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 17 April, 2019

  A Mboni za Yehova 8 anawatsekera m’ndende atakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

 2. November 2013

  A Mboni 18 anawatsekera atakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

 3. 24 April, 2002

  Mmodzi wa akuluakulu a boma anatsimikiza kuti dziko la Singapore siliona kuti munthu ali ndi ufulu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

 4. February 1995

  A Mboni za Yehova omwe ndi nzika za dziko la Singapore anayamba kuzunzidwa komanso kumangidwa kwambiri.

 5. 8 August, 1994

  Khoti Lalikulu ku Singapore linakana apilo yomwe a Mboni anapanga.

 6. 12 January, 1972

  Boma la Singapore linachotsa chipembedzo cha Mboni za Yehova m’kaundula wawo wa zipembedzo.