Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

SINGAPORE

Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Boma la Singapore likumanga anyamata a Mboni za Yehova chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Mu 1967, boma la Singapore linakhazikitsa lamulo lolola anthu kukana kulowa usilikali chifukwa cha kudwala kapena zifukwa zina. Koma lamuloli sililola anthu kukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Dziko la Singapore limakakamiza anthu kulowa usilikali ndipo silipatsa anthu ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Izi zikupangitsa kuti a Mboni azimangidwa n’kumakhala kundende kwa miyezi 39.

Mnyamata wa Mboni akafika zaka 18, amakakamizidwa kulembetsa usilikali. Akakana, amamangidwa ndipo amakakhala kundende kwa miyezi 15. Miyeziyi ikatha, amatulutsidwa ndipo nthawi yomweyo amauzidwa kuti avale yunifolomu ya usilikali n’kuyamba kuphunzira usilikali. Akakananso zimenezi, amapititsidwa kundende n’kukakhalako miyezi 24.

Boma la Singapore Likukana Kutsatira Malamulo a Bungwe la United Nations

Kwa nthawi yaitali, Bungwe la United Nations lakhala likulimbikitsa mayiko omwe ndi mamembala a bungweli kuti “asamaiwale zoti munthu akamakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira amakhala akugwiritsa ntchito ufulu wonena maganizo ake, ufulu wotsatira chikumbumtima komanso ufulu wachipembedzo womwe uli mu chikalata cha mfundo za ufulu wachibadwidwe cha Universal Declaration of Human Rights.” Ngakhale kuti dziko la Singapore linakhala membala wa bungwe la United Nations mu 1965, likukana kugwirizana ndi bungweli pa nkhani imeneyi. Pa April 24, 2002, mkulu wa boma la Singapore analembera kalata komiti ya bungwe la United Nations yoona za ufulu wa anthu. Iye analemba kuti: “Zikhulupiriro komanso zochita za munthu zikakhala kuti zikusemphana ndi ufulu wa dziko lino wokhazikitsa chitetezo, munthuyo ayenera kutsatira lamulo la dziko lokhudza chitetezo.” Mkuluyu anapitiriza kuti: “Ife sitikuona kugwirizana kwa ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira ndi mfundo zokhudza ufulu wa anthu.”

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. December 12, 2014

  A Mboni za Yehova 19 ali m’ndende chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupira. M’modzi pa anthu amenewa anakana kuti dzina lake liikidwe pa m’ndandanda ya asilikali amene angaitanidwe pa nthawi ina iliyonse.

 2. September 16, 2014

  A Mboni za Yehova 15 ali m’ndende chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupira. M’modzi pa anthu amenewa anakana kuti dzina lake liikidwe pa m’ndandanda ya asilikali amene angaitanidwe pa nthawi ina iliyonse.

 3. July 30, 2014

  A Mboni 16 anaikidwa m’ndende yoyang’aniridwa ndi asilikali chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

 4. November 2013

  A Mboni 18 anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

 5. April 24, 2002

  Mkulu wa boma ananena kuti dziko la Singapore silipatsa munthu ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

 6. February 1995

  A Mboni za Yehova ambiri omwe ndi nzika za dziko la Singapore anayamba kuzunzidwa komanso kumangidwa kwambiri.

 7. August 8, 1994

  khoti lalikulu la ku Singapore linakana apilo ya a Mboni za Yehova.

 8. January 12, 1972

  Boma la Singapore linalamula kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi chosavomerezeka m’dzikoli.