Pitani ku nkhani yake

27 SEPTEMBER, 2016
RUSSIA

Tsiku Lomvetsera Mlandu Wokhudza Kutseka Likulu la a Mboni ku Russia Alisinthanso

Tsiku Lomvetsera Mlandu Wokhudza Kutseka Likulu la a Mboni ku Russia Alisinthanso

Pa 23 September, 2016, khoti lina la m’boma la Tver mu mzinda wa Moscow ku Russia, linanena kuti lasintha tsiku loti lidzamvetsere nkhani yomwe a Mboni a m’dzikolo anachita apilo ku khotilo. Nkhaniyo ndi yokhudza kalata yowopseza yochokera ku ofesi ya Woimira Boma pa Milandu yonena kuti akufuna kutseka likulu la a Mboniwo m’dzikolo. Pa 20 September, 2016, ofesi ya Woimira Boma pa Milandu inakapereka ku khotiko kalata ya masamba 200 yotsutsa apilo ya a Mboniwo. Chifukwa cha zimenezi, a Mboniwo anapempha khotilo kuti liwapatse nthawi yoti awerenge kalatayo mofatsa. Woweruza milandu pa khotilo anena kuti mlanduwu adzapitiriza kuuzenga pa 12 October, 2016. Pa nthawiyi khotilo lidzaunikanso nkhani imene a Mboni anachita apiloyi komanso ngati zimene anachita Woimira Boma pa Milandu poopseza kuti atseka likululo zili zogwirizana ndi malamulo.