Mlandu umene a Mboni anaimbidwa ku Taganrog ukusonyeza kuti anthu am’dzikoli amatsutsa kwambiri chipembedzo cha Mboni za Yehova. Posachedwapa, woweruza mlanduwu apereka chigamulo. Kodi dziko la Russia litsekera m’ndende nzika zake chifukwa chongochita zinthu zachipembedzo chawo mwamtendere? M’vidiyoyi a Gajus Glockentin, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Europe, akupempha kuti dziko la Russia lizichita zinthu mwachilungamo komanso kulemekeza ufulu wa anthu wachipembedzo.