Pitani ku nkhani yake

JULY 4, 2014
RUSSIA

A Mboni za Yehova Akuimbidwa Mlandu ku Taganrog

A Mboni za Yehova Akuimbidwa Mlandu ku Taganrog

Mlandu wa anthu 16 a Mboni za Yehova a ku Taganrog m’dziko la Russia, omwe tsopano watha miyezi 14 unazengedwanso mwezi wa July 2014. Pa nthawi yozenga mlanduwu, khoti linaona maumboni 60 omwe ambiri anali okhudza misonkhano, mapemphero komanso mawu a m’Baibulo ndipo zonsezi zinachita kujambulidwa. Misonkhanoyi ndi imene a Mboni za Yehova padziko lonse amakhala nayo.

Mlanduwu ukhoza kupangitsa kuti a Mboni amene akuimbidwa mlanduwa komanso ena 800 omwe ali mumzindawu asakhalenso ndi ufulu wa kulambira. Anthu 16 onse amene akuimbidwa mlanduwa anenetsa kuti sasiya zimene amakhulupirira ndipo kaya khoti ligamula zotani, iwo apitiriza kukhala a Mboni za Yehova.

Vidiyoyi ikusonyeza anthu ena amene akuimbidwa mlanduwu komanso maloya awo. Iwo akuyesetsa kumenyera ufulu wawo wolambira ndipo akuchita zimenezi ngakhale kuti akuimbidwa mlandu mopanda chilungamo.