Mlandu wa a Mboni za Yehova okwana 16 a ku Taganrog m’dziko la Russia womwe unayamba mu February 2015, watha miyezi 5 tsopano uli kukhoti. A Mboni akumangidwa ndiponso kulipiritsidwa ndalama chifukwa chongochita zimene amakhulupirira basi.

Mlanduwu unayamba kuzengedwa pa 13 May, 2013 atauzidwa kuti ndi olakwa chifukwa chochita zimene dziko la Russia limaona kuti ndi zonyanyira ndiponso zosokoneza maganizo a anthu. Khotili linagamula kuti a Mboni 7 alipire ndalama ndipo linagamulanso kuti a Mboni 4 akakhale m’ndende kwa nthawi yaitali. Koma woweruzayo ananena kuti anthuwa asalandire kaye chilango chawochi. Pa December 12, 2014, khothi la apilo linalamula kuti mlanduwu uzengedwenso pomvera pempho la amene ankaimira boma pa mlanduwu. A Mboni za Yehova akuyembekezera kumva chigamulo chatsopano pa mlanduwu kumapeto kwa mwezi wa June.