Pitani ku nkhani yake

JULY 21, 2015
RUSSIA

Akuluakulu a Unduna Woona za Katundu Wolowa ndi Kutuluka M’dziko la Russia Analetsa Kuti Mabaibulo Asalowe M’dzikolo

Akuluakulu a Unduna Woona za Katundu Wolowa ndi Kutuluka M’dziko la Russia Analetsa Kuti Mabaibulo Asalowe M’dzikolo

Pa 14 July 2015, akuluakulu a unduna woona za katundu wolowa ndi kutuluka m’dziko la Russia anachita zinthu zodabwitsa kwambiri kwa a Mboni za Yehova. Akuluakulu a undunawu analetsa kuti a Mboniwo asalowetse m’dzikolo Mabaibulo a Dziko Latsopano a chilankhulo cha Chirasha. Kuyambira mu March 2015, dziko la Russia linaletsa kuti a Mboni asamalowetse m’dzikolo mabuku onse a chipembedzo chawo. Akuluakulu a undunawu analetsa kuti mabukuwo asalowe ngakhale kuti kulowetsa mabukuwo si koletsedwa m’dzikolo. Zimene dzikoli lachita poletsa mabuku a Mboni kulowa m’dzikolo ndiponso kutseka webusaiti yawo ya www.jw.org, zikusonyezeratu kuti anthu alibe ufulu wolambira, wolankhula ndiponso wolemba zinthu.