Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

NOVEMBER 28, 2014
RUSSIA

Kodi Khoti la Rostov Ligamula Zotani pa Mlandu Umene a Mboni za Yehova Apanga Apilo?

Kodi Khoti la Rostov Ligamula Zotani pa Mlandu Umene a Mboni za Yehova Apanga Apilo?

Pa December 11, 2014, khoti la m’chigawo cha Rostov lidzamvetsera mlandu womwe a Mboni za Yehova 16 a ku Taganrog, m’dziko la Russia anachita apilo. Iwo anaimbidwa mlandu chifukwa chokonza komanso kupanga misonkhano ya chipembedzo chawo yomwe anaichita mwamtendere.

Zinthu zinayamba kusokonekera mu 2011, pamene akuluakulu a boma amakafufuza mabuku a Mboni m’nyumba zawo komanso kujambula mawu a nkhani za misonkhano yawo mwachinsinsi. Izi zinapangitsa kuti a Mboni aimbidwe milandu yoti anaphwanya malamulo. Pa July 30, 2014, khoti la mumzinda wa Taganrog linagamula kuti a Mboni za Yehova 7 ndi olakwa. Apa n’kuti ataimbidwa mlandu kwa miyezi 15. Woweruza analamula a Mboni onse 7 kuti apereke chindapusa cha ndalama zambiri ndipo analamula anthu 4 pa anthu 7 amenewa kuti akakhale kundende popanda kuwauza nthawi yotulukira. Koma nthawi yomweyo anasintha n’kunena kuti asalipirenso ndalamazo komanso kuti enawo asapite kundende. woweruzayo ananenanso kuti a Mboni 9 pa a Mboni 16 aja alibe mlandu koma anangochita nawo zinthu zosokoneza maganizo a anthu zomwe ndi zoletsedwa m’dzikolo. A Mboni onse 16 apanga apilo ndipo akupempha kuti asaimbidwe mlandu uliwonse.

Nayenso woimira boma pa milandu anapanga apilo ndipo analamula khoti la Rostov kuti a Mboni 4 akatsekeredwe kundende pamapeto pa mlanduwu. Analamulanso kuti khotilo lisinthe chigamulo chimene linapereka chakuti a Mboni 9 ndi osalakwa ndipo ligamule kuti anthuwo ali ndi mlandu wochita zinthu zosokoneza maganizo a anthu zomwe ndi zoletsedwa m’dzikolo.

A Vasiliy Kalin omwe ndi oimira ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko la Russia, anati: “Ndikukhulupirira kuti khoti la Rostov liona zinthu zopanda chilungamo zimene zachitikira a Mboni 16 ndipo ligamula kuti ndi osalakwa.”