Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

6 APRIL, 2017
RUSSIA

Khoti Lalikulu M’dziko La Russia Lipitiriza Mlandu Wofuna Kuletsa Mboni Za Yehova M’dzikolo pa 7 April

Khoti Lalikulu M’dziko La Russia Lipitiriza Mlandu Wofuna Kuletsa Mboni Za Yehova M’dzikolo pa 7 April

Khoti Lalikulu m’dziko la Russia lero layamba ndi kumvetsera Unduna Woona Zachilungamo womwe ukuti mabungwe onse a Mboni za Yehova m’dzikolo ndi oyeneradi kutsekedwa chifukwa makhoti ang’onoang’ono ananena kuti mabungwewo ankachita zinthu zoopsa. Kenako woweruza anafunsa oimira Undunawo kuti afotokoze mmene zochita za mabungwe 8 a Mboni m’dzikolo zikutsimikiziradi kuti Ofesi ya Nthambi ya Mboni m’dzikolo komanso mabungwe onse 395 a Mboni za Yehova ayenera kutsekedwa. Woweruza anafunanso kudziwa kuti kutsekedwa kwa mabungwewa kukhudza bwanji kulambira kwa Mboni za Yehova, iye anafunsanso mobwerezabwereza kuti a Mboni amachita zinthu zotani zomwedi zikutsimikizira kuti amaopseza chitetezo cha anthu a m’dzikolo. Maloya oimira Mboni za Yehova pamlanduwu anafunsa mafunso omwe anasonyeza kuti Unduna Woona za Chilungamo ukufunadi kutseka chipembedzo cha Mboni za Yehova osati kungotseka mabungwe awo omwe ndi ovomerezedwa ndi boma la Russia.

Mlanduwu upitirizidwa pa 7 April, 2017, nthawi ya 10:00 m’mawa.