Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

APRIL 13, 2016
RUSSIA

Milandu Yolimbana ndi a Mboni Yomwe Yachitika Posachedwa M’dziko la Russia

Milandu Yolimbana ndi a Mboni Yomwe Yachitika Posachedwa M’dziko la Russia
  • Taganrog, Chigawo cha Rostov. Pa 17 March, 2016, khoti la ku Rostov linagwirizana ndi zomwe khoti lina laling’ono linagamula kuti a Mboni ena 16 ndi olakwa chifukwa chochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo. Komabe khotilo linachepetsa ndalama za chindapusa zomwe a Mboni okwana 12 mwa anthuwa analamulidwa kupereka kufika pa madola 147 a ku America. Cholinga chenicheni chimene ayimitsira kaye kuti anthuwa asapite kundende komanso chimene achepetsera ndalamazo, sichikudziwika.

  • Woimira boma pa milandu akufuna kuti Baibulo likhale m’gulu la zinthu zoopsa. Woimira boma pa milandu wa ku Leningrad-Finlyandskiy analemba chisamani ndi cholinga choti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika likhale m’gulu la zinthu zoopsa. Baibuloli limafalitsidwa ndi a Mboni za Yehova. Zimenezi ndi zosemphana kwambiri ndi zimene Gawo 3-1 la Lamulo Lolimbana ndi Zinthu Zoopsa limanena. Gawoli limanena kuti lamulo lolimbana ndi zinthu zoopsa siliyenera kugwiritsidwa ntchito pa Baibulo. Ngakhale kuti n’zosachita kufunsa kuti Baibulo la Dziko Latsopano ndi Baibulo, woimira boma pa milanduyo ananena kuti anachita zimenezo chifukwa chakuti ma Baibulo okhawo amene anamasuliridwa mogwirizana ndi “miyambo yopatulika” ya Tchalitchi cha Orthodox cha ku Russia, ndi amene akuyenera kutchedwa ma Baibulo. Khoti la mumzinda wa Vyborg lidzazenganso mlanduwu pa 26 April, 2016.