Pitani ku nkhani yake

RUSSIA

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Akuluakulu a boma la Russia akupitirizabe kulimbana ndi a Mboni za Yehova powachitira zankhanza zofanana ndi zomwe ankakumana nazo m’nthawi ya ulamuliro wa Soviet. Pofika pa 18 February, 2019, a Mboni 26 anali atatsekeredwa m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu, 26 ali paukaidi wosachoka panyumba ndipo enanso 46 sakuloledwa kuchoka komwe amakhala. Onse akuimbidwa mlandu wochita nawo zinthu zoopsa, wotsogolera gulu lochita zinthu “zoopsa,” kapena kupereka ndalama zothandizira gululi. A Mboni osachepera 140 panopa akufufuzidwa ngati anapalamula milandu.

Mu July 2018, akuluakulu a boma ku Omsk anatsekera m’ndende wa Mboni woyamba wamkazi poyembekezera kumuzenga mlandu ndipo zimenezi n’zochititsa mantha chifukwa akazi enanso akhoza kumangidwa. Ngakhale kuti panopa anatulutsidwa ndipo ali paukaidi wosachoka panyumba, patatha miyezi yochepa, mu October 2018, apolisi anamanga akazi atatu a Mboni mumzinda wa Sychevka. Iwo adakali m’ndende poyembekeza kuwazenga milandu ndipo sawatulutsa mpaka pa 19 May, 2019.

Akuluakulu a bomawa amati amachita zimenezi potengera chigamulo cha mu April 2017 chomwe chinachititsa kuti mabungwe a Mboni atsekedwe, komanso akugwiritsa ntchito molakwika Gawo 282 la m’Buku la Malamulo a Zaupandu. Koma zoona zake n’zoti a boma akuzenga milandu a Mboni za Yehova chifukwa cholambira Mulungu mwamtendere. Ngati angawapeze olakwa, ena mwa a Mboni omwe anamangidwa akhoza kulamulidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka mpaka 10.

Kungoyambira mu February 2018, apolisi akhala akumanga ndi kutsekera m’ndende a Mboni za Yehova. Apolisi onyamula mfuti akhala akulowa m’nyumba za a Mboni ndipo nthawi zambiri akapezamo anthu, ana ndi achikulire omwe, amawaloza ndi mfuti m’mutu n’kuwakakamiza kuti agone pansi. Akamachita chipikisheni m’nyumbazo, amalanda zinthu za a Mboniwo komanso kutengera a Mboni ena kupolisi kuti akapitirize kuwafunsa mafunso. Kenako apolisiwo amatsegulira milandu a Mboni ena powaganizira kuti anachita zinthu zoopsa ndipo amapempha makhoti kuti awatsekere m’ndende poyembekezera kuzenga milandu yawo. A Mboni akatsekeredwa, apolisi amapempha makhotiwo kuti awonjezere nthawi yoti akhale m’ndendemo ndipo nthawi zambiri makhoti amachitadi zimenezi.

Pa 15 February, 2019, zinthu zankhanza kwambiri zinachitika mumzinda wa Surgut. Apolisi anachitira nkhanza a Mboni 7 aamuna pambuyo pochita chipikisheni m’nyumba za a Mboni mumzindawu. Anawavula zovala zawo zonse, kuwabanikitsa, kuwathira madzi, kuwamenya, komanso anawagwiritsa shoko kumatako. Zankhanzazi zinachitikira mu ofesi ya komiti ya ofufuza milandu mumzinda wa Surgut. A Mboni 19 (mmodzi wamkazi) akufufuzidwa pa milandu ‘yotsogolera zochita za gulu loopsa.’ Amuna atatu mwa omwe anachitidwa nkhanzazi adakali m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

Mlandu wa a Dennis Christensen Unaweruzidwa Mopanda Chilungamo

A Dennis Christensen omwe ndi azaka 46 komanso ndi nzika ya dziko la Denmark, anakhala akuimbidwa mlandu pafupifupi chaka chimodzi ndipo anakaonekera m’khoti maulendo oposa 50. Iwo anagamulidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka 6 chifukwa chochita zinthu zomwe amakhulupirira monga wa Mboni za Yehova. Pa 6 February, 2019, woweruza milandu wa khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy ku Oryol dzina lake Aleksey Rudnev, anawerenga chigamulo chomwe chinanena kuti a Christensen ndi olakwa pa mlandu wabodza ‘wotsogolera zochita za gulu loopsa,’ zomwe n’zosemphana ndi Gawo 282.2(1) m’Buku la Malamulo a Zaupandu a boma la Russia. Maloya a a Christensen akupanga apilo chigamulochi.

A Christensen anamangidwa pa 25 May, 2017, pomwe apolisi onyamula mfuti ndiponso anthu oimira gulu lachitetezo la Federal Security Services, anakasokoneza msonkhano wachipembedzo womwe a Mboni za Yehova ankachita mwamtendere umenenso a Christensen ankachita nawo. Kungoyambira nthawi imeneyo, iwo akhala akusungidwa m’ndende ya Detention Facility No. 1 ku Oryol.

Ntchito Yofuna Kuthetsa Mchitidwe Wotsekera M’ndende Anthu Osalakwa Ikupitirira

Nkhanza zimene apolisi akupitirizabe kuchitira a Mboni za Yehova ku Russia zikusonyeza kuti cholinga chawo sikungotseka mabungwe ovomerezeka a Mboni, koma kuwaletsa kulambira. Maloya a a Mboni osalakwawa anayesetsa kuti athetse mchitidwe wotsekera m’ndende a Mboni mopanda chilungamo, koma zimenezi sizinathandize. Choncho maloyawa anakadandaula za nkhaniyi ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu komanso ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka ndiponso anapanga apilo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. A Mboni za Yehova padziko lonse akuyembekezera kuti makhoti a m’mayiko ena achitapo kanthu posachedwapa kuti athetse nkhanza zomwe boma la Russia likuchita powaphwanyira ufulu wawo wopembedza.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 18 February, 2019

  A Mboni okwana 26 anatsekeredwa m’ndende.

 2. 15 February, 2019

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni m’mizinda ya Surgut ndi Lyantor yomwe ili m’dera loima palokha la Khanty Mansi. A Mboni atatu aamuna anamangidwa n’kuwatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

 3. 6 February, 2019

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni mumzinda wa Uray. Bambo mmodzi wa Mboni anamangidwa n’kumutsekera m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu.

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni mumzinda wa Saransk. A Mboni atatu aamuna anamangidwa n’kuwatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

  Khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy linanena kuti a Dennis Christensen ndi olakwa ndipo linagamula kuti akhale m’ndende kwa zaka 6.

 4. 27 January, 2019

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni mumzinda wa Ivanovo. Bambo mmodzi wa Mboni anamangidwa n’kuikidwa m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu.

 5. 12 December, 2018

  Apolisi mumzinda wa Neftekumsk anamanga bambo wina wa Mboni atangofika kupolisi komwe anapita apolisiwo atamuitanitsa.

 6. 9 December, 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni ku Neftekumsk. Azibambo awiri a Mboni anawamanga n’kuwatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu.

 7. 10 November, 2018

  Apolisi anafika pamalo ena odyera ndipo anasokoneza anthu omwe ankadya pamalopo. Iwo anamanga azibambo ambiri a Mboni n’kuwatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

 8. 9 November, 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za anthu ku Novosibirsk ndipo anamanga bambo mmodzi wa Mboni n’kumutsekera m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu.

 9. 18 October, 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za anthu ku Dyurtuli ndipo anamanga bambo mmodzi wa Mboni n’kumutsekera m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu.

 10. 9 October, 2018

  Apolisi komanso gulu la apolisi apadera anathyola n’kulowa m’nyumba za anthu ku Kirov. Azibambo ambiri a Mboni, kuphatikizapo a Andrzej Oniszczuk omwe ndi nzika ya dziko la Poland, anamangidwa n’kutsekeredwa m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

 11. 7 October, 2018

  Apolisi komanso gulu la apolisi apadera anathyola n’kulowa m’nyumba za anthu ku Sychevka ndipo anamanga a Nataliya Sorokina ndi a Mariya Troshina. Azimayi awiriwa anawatsekera m’ndende pa mpaka pa 19 February, 2019, pomwe akuyembekezeka kudzawazenga milandu. Tsopano pali azimayi atatu ku Russia omwe anamangidwa pa milandu yochita zinthu zoopsa, ndipo ena ndi a Anastasiya Polyakova omwe anamangidwa mu July.

 12. 2 August, 2018

  Apolisi komanso akuluakulu a FSB anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni ku Khabarovsk ndipo anamanga bambo wina wa Mboni n’kutsekera bambowa m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu.

 13. 28 July, 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba ya mayi a bambo wina wa Mboni omwe ndi achikulire n’kumanga bambowo. Iwo anawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu.

 14. 25 July, 2018

  Gulu linalake la apolisi olimbana ndi zachipolowe ku Russia (Special Rapid Response Unit of the Russian National Guard) linathyola n’kulowa m’nyumba za anthu ku Kostroma. Bambo wina wa Mboni anamangidwa ndi kutsekeredwa m’ndende poyembekezera kuzengedwa mlandu.

 15. 22 July, 2018

  Apolisi ndi akuluakulu a FSB anathyola n’kulowa m’nyumba za anthu ku Berezovskiy. Azibambo awiri a Mboni anamangidwa n’kuwatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

 16. 15 July, 2018

  Apolisi anachita chipikisheni m’nyumba za a Mboni ambiri ku Penza. Bambo wina wa Mboni anamangidwa n’kutsekeredwa m’ndende poyembekezera kuzengedwa mlandu.

 17. 4 July, 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni ku Omsk. A Sergey ndi a Anastasiya Polyakov anamangidwa ndipo anawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu. Mayi Polyakov ndi wa Mboni wamkazi woyamba kumangidwa ku Russia pa mlandu wochita zinthu zoopsa.

 18. 3 July, 2018

  Apolisi anamanga a Andrey Stupnikov pabwalo lina la ndege ku Krasnoyarsk ndipo anawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu.

 19. 12 June, 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni ku Saratov. Azibambo angapo a Mboni anamangidwa ndipo anawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

 20. Chakumayambiriro kwa June 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni ku Tomsk ndi ku Pskov. Bambo wina wa Mboni anamangidwa ndi kutsekeredwa m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu.

 21. May 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni ku Orenburg, Birobidzhan, Perm, Naberezhnye Chelny, Magadan, komanso ku Khabarovsk. Azibambo a Mboni okwana 10 anamangidwa n’kuwatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

 22. April 2018

  Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni ku Ufa, Polyarny, Vladivostok, ndi ku Shuya. Azibambo ambiri a Mboni anamangidwa ndi kutsekeredwa m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.

 23. 19 February, 2018

  Kuzenga mlandu wa a Dennis Christensen kunayamba pakhoti la m’boma la Zheleznodorozhniy ndipo woweruza milandu wina dzina lake Aleksey Rudnev ndi amene ankazenga mlanduwu.

 24. 20 July, 2017 mpaka November 2018

  Nthawi yoti a Dennis Christensen awasunge m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu inawonjezeredwa maulendo angapo. Koyamba inawonjezeredwa ndi khoti la m’boma la Sovietskiy ndipo kenako inawonjezeredwa ndi khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy.

 25. 26 May, 2017

  Khoti la m’boma la Sovietskiy ku Oryol linagamula kuti a Dennis Christensen akhale m’ndende kwa miyezi iwiri poyembekezera kuwazenga mlandu.

 26. 25 May, 2017

  Apolisi anasokoneza misonkhano ya a Mboni ku Oryol ndipo anamanga a Dennis Christensen.