Pa May 27, 2015, unduna woona zachilungamo m’dziko la Russia unavomereza bungwe la Mboni za Yehova mumzinda wa Moscow. Izi zachitika patatha zaka pafupifupi 5 kuchokera pamene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linanena kuti zimene khoti la ku Moscow linagamula zothetsa bungwe la Mboni za Yehova zinali zosagwirizana ndi malamulo.

Mu 2004 khoti lotchedwa Golovinskiy la mumzinda wa Moscow linagamula kuti bungwe la Mboni za Yehova lithetsedwe. Chigamulochi chinaperekedwa patapita zaka zambiri mlanduwu ukukambidwa. M’chaka cha 2010, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linalamula boma la Russia kuti lisathetse bungweli komanso kuti lipereke chindapusa. Boma la Russia linapereka ndalamazi koma lavomereza bungweli pompano.