Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

OCTOBER 26, 2016
RUSSIA

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Likupitiriza Kuletsa Mboni za Yehova Kulambira M’dzikolo

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Likupitiriza Kuletsa Mboni za Yehova Kulambira M’dzikolo

Pa 18 October 2016, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linavomereza zimene khoti lina m’dzikolo linagamula zoti bungwe la Mboni za Yehova lovomerezeka ndi boma la mumzinda wa Orel lithetsedwe. Khotilo linanena kuti a Mboniwo amachita zinthu monyanyira komanso mosemphana ndi malamulo a boma. Bungwe la Mboni za Yehova la ku Orel, ndi la nambala 7 kuthetsedwa ndi makhoti a ku Russia. Mabungwe onsewo anathetsedwa akuluakulu a boma atagwiritsa ntchito molakwika lamulo lokhudza kuchita zinthu monyanyira pofuna kulimbana ndi a Mboni za Yehova.

M’buyomu akuluakulu a boma mumzinda wa Orel akhala akugwiritsa ntchito umboni wabodza poyesetsa kuti athetse bungwe la Mboni za Yehova la mumzindawo. Zimenezi zitalephereka, unduna woona zachilungamo unalemba chikalata mu May 2016. Chikalatachi chinali chonena kuti bungwe la Mboni za Yehova ndi gulu la anthu amene amachita zinthu monyanyira komanso mosemphana ndi malamulo a boma.

Zimene zinachitika ku Orel zinali zapadera chifukwa kanali koyamba kuti bungwe la Mboni za Yehova lithetsedwe pambuyo poti lachenjezedwa. Zili choncho chifukwa mu March 2016 bungweli lisanathetsedwe, loya wamkulu wa boma anatumiza chikalata chochenjeza kaye bungwe la Mboni za Yehova mumzindawo.