Akuluakulu a boma la Russia akulimbikirabe zofuna kulanda maofesi a ku Likulu la Mboni za Yehova ku Solnechnoye kufupi ndi St. Petersburg.

Pa 20 April 2017, Khoti Lalikulu Kwambiri linagamula kuti mabungwe onse a Mboni za Yehova atsekedwe, nyumba zomwe amagwiritsa ntchito zilandidwe kuphatikizaponso maofesi a ku likulu lawo. Koma ngakhale zili choncho, maofesiwa ali m’manja mwa bungwe la ku United States la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Loya wa boma akuyesetsa kupeza njira yoti aphwanye pangano la zaka 17, lomwe boma la Russia linasainira potsimikizira kuti maofesiwa ndi a bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Kuchokera nthawi imeneyo zonse zakhala zikuyenda bwino ndipo bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania lakhala likupereka misonkho ku boma la Russia mpaka pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linapereka chigamulo chotseka maofesi a Mboni. Panopa akuluakulu a bomawa akusakasaka njira zosavomerezeka pofuna kuti pakhale lamulo lowalola kulanda maofesi a a Mboni.

Pa 29 November, 2017, khoti linayamba kumvetsera mlanduwu koyamba ndipo woweruza anakana madandaulo omwe maloya oimira Mboni za Yehova anapereka. Zimenezi zinapereka mwayi kwa loya wa boma kuti apitirize kuwaimbabe mlandu. Kuwonjezera pa mfundo yoti nyumbazi ndi za ndalama zokwana madola mamiliyoni, zimagwiritsidwanso ntchito ngati malo okhala kwa anthu 400 omwe ndi nzika za ku Russia komanso za mayiko ena. Ndipotu ena mwa anthuwa akhala pamalowa kwa zaka zoposa 20. Panopa a Mboni akukhala mwamantha, chifukwa chodera nkhawa kuti asamutsidwa ku likululi komanso kuti utumiki wawo wongodzipereka pofuna kuthandizana ndi abale awo a ku Russia usokonezedwa.

Khoti lidzayamba kumvetsera maumboni enanso a mlanduwu pa 7 December, 2017, nthawi ya 2:00 masana ku khoti la m’dera la Sestroretskiy ku St. Petersburg.