Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

APRIL 13, 2016
RUSSIA

Akuluakulu a Dziko la Russia Akuchita Zonse Zomwe Angathe Pofuna Kuthetsa Mabungwe a Mboni za Yehova M’dzikolo

Akuluakulu a Dziko la Russia Akuchita Zonse Zomwe Angathe Pofuna Kuthetsa Mabungwe a Mboni za Yehova M’dzikolo

M’madera ambiri a m’dziko la Russia, akuluakulu a boma akupitiriza kulimbana ndi a Mboni za Yehova ponena kuti zinthu zimene anachita zokhudza chipembedzo chawo ndi zoopsa.

  • Dera la Tyumen. Ofesi ya oimira boma pa milandu inanena kuti wa Mboni wina wa m’dera la Tyumen ndi wolakwa chifukwa chogawira anthu mabuku omwe iwo amati ndi oopsa. Khoti litagamula kuti wa Mboniyo ndi wolakwa, woimira boma pa milanduyo ananena kuti gulu la Mboni za Yehova liyenera kuthetsedwa m’deralo. Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia lidzayamba kumva za nkhaniyi pa 14 April, 2016.

  • Elista, Republic of Kalmykia. Mkulu wa apolisi m’dera la Elista analamula kuti achite chipikisheni mu Nyumba ya Ufumu ya m’derali ndipo anapeza mabuku a Mboni amene dziko la Kalmykia limati ndi oopsa. Pogwiritsa ntchito umboni wabodza, woimira boma pa milandu wa m’dzikoli anadula chisamani choti bungwe la Mboni za Yehova ku Elista lithetsedwe. Khoti Lalikulu Kwambiri m’dziko la Russia liyamba kumva za nkhaniyi posachedwapa.

  • Posachedwapa Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia likuyembekezera kumvanso nkhani ya kuthetsedwa kwa mipingo ya Mboni za Yehova ku Stariy Oskol komanso ku Belgorod.