A mu Ofesi ya Woimira Boma pa Milandu ku Russia alemba kalata yowopseza kuti atseka likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo chifukwa amachita zinthu zokhudza chipembedzo chawo. Izitu n’zodabwitsa chifukwa a Mboni amachita zimenezi padziko lonse ndipo amazichita mwamtendere. Kalatayi yomwe inalembedwa pa 2 March, 2016, inasainidwa ndi wachiwiri kwa woimira boma pamilandu a V. Ya. Grin, ndipo m’kalatayi iwo ananena kuti a Mboni za Yehova amachita “zoopsa” komanso “zophwanya malamulo.” Ananenanso kuti boma litseka maofesi a Mboniwo ngati pomatha miyezi iwiri sasiya kuphwanya malamulo.

Boma la Russia ndi limene likukonza zoti maofesi a Mboni za Yehova atsekedwe m’dzikolo. Kuyambira mu 2007, akuluakulu a boma akhala akugwiritsa ntchito molakwa lamulo lokhudza zinthu zoopsa polimbana ndi a Mboni za Yehova, kuthetsa mabungwe amene amawaimira pa nkhani zosiyanasiyana komanso kuletsa kuti mabuku awo asamafalitsidwe.