Pitani ku nkhani yake

APRIL 5, 2017
RUSSIA

Khoti Lalikulu la Dziko la Russia Likupitiriza Kuzenga Mlandu Wokhudza Kuletsa Ntchito za Mboni za Yehova M’dzikolo.

Khoti Lalikulu la Dziko la Russia Likupitiriza Kuzenga Mlandu Wokhudza Kuletsa Ntchito za Mboni za Yehova M’dzikolo.

Khoti Lalikulu m’dziko la Russia linaimitsa kaye mlandu wofuna kuletsa ntchito za Mboni za Yehova m’dzikolo lero, pambuyo pomvetsera ku mbali zonse zokhudzidwa ndi mlanduwu. Unduna Woona Zachilungamo m’dziko la Russia unakapereka chisamani ku Khoti Lalikulu la m’dzikolo choti “liike Ofesi ya Nthambi ya Mboni za Yehova m’dzikolo pa gulu la mabungwe amene amachita zoopsa komanso kuti ofesiyo itsekedwe. Undunawo ukufunanso kuti ntchito zonse zimene ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova imagwira ziletsedwe.” Khotili lipitiriza kuzenga mlanduwu pa April 6, 2017, nthawi ya 2:00 masana.

A Mark Sanderson, omwe ndi membala wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndipo analipo pamene mlanduwu umakambidwa, ananena kuti: “Ndi zodandaulitsa kuti Khoti Lalikulu la Dziko la Russia linatsutsa kapena kukana kumvetsera umboni woperekedwa ndi Ofesi ya Nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dzikolo. Akazembe a m’mayiko osiyanasiyana komanso mabungwe omenyera ufulu wa anthu analipo pa mlanduwu. Aliyense akudzionera yekha mmene nkhaniyi ikuyendera.”