Pitani ku nkhani yake

23 NOVEMBER, 2017
RUSSIA

Khoti la ku Russia Likuyembekezeka Kudzamvetsera Apilo ya Mboni za Yehova Yotsutsa Kuti Baibulo Lawo ndi “Loopsa”

Khoti la ku Russia Likuyembekezeka Kudzamvetsera Apilo ya Mboni za Yehova Yotsutsa Kuti Baibulo Lawo ndi “Loopsa”

Pa 6 December 2017, khoti la ku Leningrad lidzamvetsera apilo yomwe a Mboni anachita potsutsa chigamulo chomwe khoti lina laling’ono linapereka chonena kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la m’Chirasha liletsedwe.

Mu August 2017, khoti la mumzinda wa Vyborg linagwirizana ndi zimene loya wa boma ananena kuti Baibulo la Dziko Latsopano silikuyenera kutchedwa Baibulo. Loyayo ananena izi chifukwa choti m’Baibuloli muli dzina la Mulungu lakuti Yehova, lomwe linamasuliridwa kuchokera ku zilembo 4 za Chiheberi. Loya wa bomayu ananena izi pofuna kuzemba lamulo lokhudza kuletsa zinthu zoopsa lomwenso limaletsa kutchula mabuku opatulika kuti ndi zinthu zosokoneza.

A Mboni za Yehova omwe amafalitsa Baibulo la Dziko Latsopano la chinenero cha Chirasha akutsutsa mwamphamvu chigamulo chimene khoti la mumzinda wa Vyborg linapereka choti Baibulo lawo ndi “loopsa.” Baibulo la Dziko Latsopano limafalitsidwa lathunthu kapena mbali yake chabe m’zinenero 161. Baibuloli linamasuliridwa molondola, ndi losavuta kuwerenga ndipo anthu ambiri amalikonda. Pofika pano Mabaibulo oposa 200 miliyoni afalitsidwa kale.