Pa 20 July, 2017, khoti la Sovietskiy lomwe lili m’boma la Oryol linawonjezera nthawi yoti a Dennis Christensen akhale m’ndende mpaka pa 23 November, 2017 ngakhale kuti mlandu wawo sunaweruzidwe. A Christensen ndi nzika ya ku Denmark ndipo ndi a Mboni za Yehova. Iwowa anamangidwa pa 25 May akuchita nawo msonkhano wachipembedzo womwe unkachitika mwamtendere. Pa nthawiyi akuluakulu oona za chitetezo m’dziko la Russia limodzi ndi apolisi ovala zinthu zophimba nkhope anafika n’kudzasokoneza msonkhanowo womwe unkachitikira ku Oryol.

Maloya anapempha kuti a Christensen atulutsidwe pabelo ndipo anali okonzeka kupereka malipiro onse a beloyi. Komabe khotili linakana kupereka beloyo ngakhale kuti a Christensen alibe mbiri iliyonse yoti anapalamulapo mlandu kapena kuchita zachisokonezo.

Khotili linawonjezera nthawi ya a Christensen pambuyo poti pa 17 July, khoti lalikulu la apilo la m’dziko la Russia lanena kuti silinasinthe chigamulo chake chapoyamba chotseka maofesi a Mboni za Yehova komanso kuletsa ntchito zachipembedzo zimene a Mboni amachita m’dzikolo. Padutsa zaka zoposa 10 akuluakulu a dziko la Russia akulimbana ndi a Mboni za Yehova komanso kuwaganizira kuti ndi kagulu koopsa. Pofika pano, akuluakuluwa akwaniritsa cholinga chawo chofuna kutseka ntchito za Mboni za Yehova ponamizira kuti akuchita zimenezi pogwiritsa ntchito malamulo a m’dzikolo.

Pothirirapo ndemanga pa zomwe a Mboni za Yehova akukumana nazo ku Russia, a Kate M. Byrnes, a m’bungwe loona za chitetezo komanso mgwirizano wa mayiko a ku America komanso ku Ulaya, anati: “Tadzidzimuka kwambiri ndi chigamulo chimene chinaperekedwa ndi khoti lalikulu kwambiri pa 17 July, choti silinasinthe chigamulo chake choyamba chotseka likulu la Mboni za Yehova, mipingo yawo yokwana 395 komanso kuletseratu ntchito zawo zachipembedzo powaganizira kuti akuchita zinthu zobweretsa chisokonezo. N’zokhumudwitsa kwambiri kuti a Mboni okwana 175,000 omwe ali ku Russia akhoza kumaimbidwa mlandu ngati atawapeza akuchita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo. Boma la Russia likugwiritsa ntchito molakwika lamulo loletsa zinthu zoopsa pofuna kulimbana ndi magulu ang’onoang’ono a zipembedzo omwe amachita zinthu zawo mwamtendere.”