Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

NOVEMBER 11, 2014
RUSSIA

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Lipitiriza Kuzenga Mlandu Wokhudza Kutsekedwa kwa Bungwe la Mboni la ku Samara

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Lipitiriza Kuzenga Mlandu Wokhudza Kutsekedwa kwa Bungwe la Mboni la ku Samara

Pa November 12, 2014, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia lakonza zoti lipitirize kuzenga mlandu wa apilo wokhudza kutsekedwa kwa bungwe lovomerezeka ndi boma la Mboni za Yehova la ku Samara. Mlanduwu unayamba kuzengedwa mwezi wapitawu pa October 8. Anthu ofalitsa nkhani, akazembe a m’mayiko ena, maloya komanso a Mboni za Yehova anadzazana m’holo ya khotili kuti amvetsere mlanduwu. Kenako khotilo linaimitsa mlanduwo pambuyo pochita zinthu zina ndi zina zimene zimafunika kuchitidwa mlandu wa apilo usanayambe kuzengedwa.

A Vasily Kalin, omwe ndi oimira ofesi ya Mboni za Yehova ku Russia ananena kuti: “Sitikukayikira kuti Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia kuno, lomwe ndi lolemekezeka kwambiri, lionetsetsa kuti chilungamo chatsatiridwa pa mlanduwu komanso lichita zinthu motsatira malamulo amene boma la dimokalase limayendera. Lichita zimenezi pothetsa mlandu umene ofesi yoimira boma pa milandu inasumira a Mboni.” A Mboni za Yehova akukhulupirira kuti khotili liteteza ufulu wachipembedzo umene uli m’malamulo a boma la Russia.