Pitani ku nkhani yake

MARCH 3, 2014
RUSSIA

Khoti Lalikulu ku Russia Lakana Zoti Webusaiti ya JW.ORG Itsekedwe

Khoti Lalikulu ku Russia Lakana Zoti Webusaiti ya JW.ORG Itsekedwe

Pa January 22, 2014, oweruza atatu a khoti lalikulu ku Tver anasintha chigamulo cha khoti laling’ono choti webusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova, ya jw.org, itsekedwe. * Mosiyana ndi zimene makhoti ena ku Russia akhala akugamula pa zaka zingapo zapitazi, khoti lalikululi linatsatira malamulo ndipo linakana zimene oweruza a khoti laling’ono anagamula zoti atseke webusaitiyi.

Mavutowa anayamba pamene akuluakulu a boma la Russia, omwe akupitiriza kuzunza Mboni za Yehova, anakadandaula kukhoti lina laling’ono ku Tver (lomwe lili pa mtunda wa makilomita 160 kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa Moscow) kuti litseke webusaiti ya jw.org. Mlanduwu unazengedwa pa August 7, 2013, ndipo unatenga mphindi 25 zokha. Koma akuluakulu a Mboni za Yehova m’dzikolo sanadziwitsidwe zoti boma likuwaimba mlandu kukhoti ndipo sanapatsidwe mwayi womva mbali yawo kukhotilo. A Mboniwo anamva za nkhaniyi kudzera m’manyuzipepala ndi m’mawailesi pa September 12, 2013, patangotsala maola ochepa kwambiri kuti nthawi imene munthu amaloledwa kuchita apilo pa mlandu ithe. A Mboni za Yehova atangomva za nkhaniyi, nthawi yomweyo anachita apilo kukhoti lalikulu la ku Tver.

Khoti lalikululo linaweruza mlanduwu pa January 22, 2014. Woimira boma pa milandu yemwe anali limodzi ndi akuluakulu a ku unduna wa zachilungamo komanso ku unduna woona za m’dziko, anapempha khotili kuti ligamule zoti webusaitiyi ndi “yoopsa kwambiri” ndipo ndi yofunika kutsekedwa m’dziko lonse la Russia. Koma oweruza a khotili ananena zoti boma la Russia linaphwanya ufulu wa eni ake a webusaitiyi, omwe ndi bungwe la Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. Choncho oweruzawo analamula kuti mlanduwu uzengedwenso ndipo oimbidwa mlanduwo apatsidwe mwayi wofotokoza mbali yawo. Apatu khoti lalikululi linakana zimene akuluakulu a boma la Russia anapempha.

Akuluakulu a boma la Russia ayamba kuzunza Mboni za Yehova m’dzikolo pogwiritsa ntchito molakwika lamulo loletsa chinthu chilichonse choopsa. Kuyambira mu 2009, akuluakulu a boma la Russia anayamba kupotoza mawu enaake amene ali mu lamulo loletsa chinthu chilichonse choopsa m’dzikolo. Boma likugwiritsa ntchito lamulo limeneli pozunza anthu a Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, boma lagwiritsa ntchito lamuloli pochita zinthu zotsatirazi kwa anthu a Mboni za Yehova:

  • kumanga anthu oposa 1,600;

  • kuletsa mabuku awo 70 osiyanasiyana;

  • kulowa ndi kufufuza m’nyumba zawo zogona komanso nyumba zawo zolambiriramo zokwana 171; ndiponso

  • kusokoneza misonkhano yawo, ndipo pofika pano misonkhano imene yasokonezedwa ndi yokwana 69.

Woweruza wa kukhoti laling’ono ku Tver anagamula zoti webusaiti ya jw.org itsekedwe chifukwa akuti pawebusaitiyi panali mabuku 6 “oopsa kwambiri.” Choncho khotili linapereka chigamulo chimenechi pa August 7, 2013, potsatira lamulo loletsa chinthu chilichonse choopsa kwambiri. Kuwonjezera pamenepa, khotili linaika webusaiti ya jw.org pagulu la zinthu zoopsa kwambiri zomwe ndi zoletsedwa m’dziko lonse la Russia.

Apa zikuonekeratu kuti zimene khotili linagamula zinali zosagwirizana ndi malamulo. Zili choncho chifukwa khotili silinapereke mwayi kwa eni ake a webusaitiyi kuti achotse pawebusaitiyi mabuku onse amene boma linkati ndi “oopsa kwambiri.” Koma khoti lalikulu linamva kuti eni a webusaitiyi anali atatseka kale mbali zina za pa jw.org n’cholinga choti mabuku onse omwe boma la Russia linkati ndi “oopsa kwambiri” asamaoneke m’dzikolo. Pa chifukwa chimenechi, oweruza a khoti lalikuluwa anaona kuti palibe chifukwa chilichonse chogwirizana ndi malamulo a dziko la Russia chomwe chingachititse kuti webusaitiyi itsekedwe. Chigamulo cha khoti lalikululi sichingasinthe ngakhale kuti patsala miyezi 6 kuti achite apilo. Kombe sikuti pali malamulo okakamiza khoti kuti limvenso mlandu ngati munthu wachita apilo. Choncho khotili lingamvenso mlanduwu kapena ayi.

Kodi zimene khoti lalikulu ku Tver lagamula ndi chiyambi cha kusintha kwa zinthu ku Russia?

Padakali mavuto ambiri. Zimene khoti lalikulu ku Tver lagamula n’zosiyana kwambiri ndi zomwe makhoti ena a m’dziko lomweli la Russia akugamula pa milandu yokhudza Mboni za Yehova. Makhoti ambiri m’dzikoli amaweruza milandu mokondera ndipo amapondereza Mboni za Yehova. Ndipotu Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya (ECHR) lakhala likudzudzula dziko la Russia mobwerezabwereza chifukwa chophwanya ufulu wolambira wa anthu a Mboni za Yehova. M’malo motsatira zimene khoti la ECHR limagamula, dziko la Russia likupitirizabe kuphwanya ufulu wa anthu. Pofuna kuteteza ufulu wawo wolambira, panopa a Mboni za Yehova ku Russia anakadandaula kukhoti la ECHR pa milandu yokwana 23, yomwe khotili likuyembekezera kuiweruza.

Kodi zimene khoti lalikulu ku Tver lagamula ndi chiyambi cha kusintha kwa zinthu ku Russia? A Mboni za Yehova akungodikira kuti aone kuti boma la Russia lichita zotani pa chigamulo cha khoti lalikululi komanso pa zimene khoti la ECHR lakhala likugamula.

^ ndime 2 Makampani a Intaneti ku Russia akhoza kutseka webusaiti ya jw.org ngati khoti lingagamule kuti webusaitiyi itsekedwe. Zimenezi zingapereke mphamvu kwa akuluakulu a boma kuti aziimba mlandu munthu aliyense wotsegula kapena wouza ena kuti azitsegula webusaitiyi.