Pa 22 February 2018, Woweruza Aleksey Rudnev wa khoti la mumzinda wa Oryol anagamula kuti Dennis Christensen akhalebe m’ndende mpaka 1 August 2018 podikira kuzengedwa mlandu. A Christensen akuimbidwa mlandu wogwira ntchito ya chipembedzo chomwe boma linanena kuti chimachita zinthu zobweretsa chisokonezo. Iwo anamangidwa mu May 2017 pamene apolisi anafika pamsonkhano wachipembedzo umene a Christensen ankachita nawo.

Woweruza anayamba kumvetsera mlanduwu pa 19 February ndipo sanapereke chigamulo pa zimene maloya onse anali atapempha. Koma pa 22 February, woweruza anakana zimene maloya a a Christensen anapempha ndipo anagamula kuti a Christensen akhalebe m’ndende. Mlandu udzayamba kuzengedwa pa 26 February nthawi ya 2:30 masana.

A Mboni za Yehova padziko lonse akudera nkhawa a Christensen ndipo akupemphera kuti mkazi wawo dzina lake Irina apitirize kupirira pa nthawi imene mwamuna wake kulibe. Panopa a Christensen akhala m’ndende kwa miyezi 9.