Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Mmene Likulu la Mboni za Yehova ku Russia Limaonekera

APRIL 27, 2016
RUSSIA

Zimene Dziko la Russia Likuchita Pofuna Kutseka Likulu la Mboni za Yehova Zikusokoneza Ufulu Wawo Wolambira Mulungu Momasuka

Zimene Dziko la Russia Likuchita Pofuna Kutseka Likulu la Mboni za Yehova Zikusokoneza Ufulu Wawo Wolambira Mulungu Momasuka

Akuluakulu a boma la Russia achitanso chinthu china chachikulu pamene akupitiriza mwankhanza kulimbana ndi Mboni za Yehova. Ofesi ya Mkulu Woimira Boma pa Milandu m’dzikoli yawopseza kuti itseka likulu la a Mboniwo ponena kuti iwo amachita “zinthu zoopsa.” M’kalata yake yowopseza yomwe inalembedwa pa 2 March, 2016, Wachiwiri kwa Woimira Boma pa Milandu a V. Ya. Grin, analamula kuti likulu la a Mboni m’dzikoli lileke kuphwanya malamulo pasanathe miyezi iwiri.

Zimene boma la Russia lachita poopseza kuti litseka likulu la Mboni za Yehova, zakolezera kwambiri moto pa cholinga cha bomali chopangitsa gulu la Mboni kukhala losafunika m’dzikolo komanso kulanda ufulu wawo wopembedza. Ngati angatseke likululi, lidzakhala m’gulu la mabungwe amene dzikoli limaona kuti ndi oopsa ndipo boma lidzalanda zinthu zonse zimene a Mboni ali nazo pa likululo. Chifukwa chakuti likulu la Mboni la m’dzikoli limachita zinthu limodzi ndi mabungwe 406 amene amaimira a Mboni komanso mipingo yawo yoposa 2,500, mabungwewa komanso mipingoyo nayonso ikhoza kuthetsedwa. Zimenezi zingachititse kuti a Mboni m’dziko lonse la Russia asakhalenso ndi Nyumba za Ufumu (kapena kuti nyumba zopemphereramo) ndipo sangakhalenso ndi ufulu wochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo.

Dziko la Russia likulimbana ndi a Mboni za Yehova pogwiritsa ntchito umboni wabodza komanso kugwiritsa ntchito dala molakwika Lamulo Lolimbana ndi Zinthu Zoopsa. Mu 2015, Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu ya Bungwe la United Nations inadandaula “ndi malipoti ambiri osonyeza kuti lamulo lokhudza zinthu zoopsa likupitirirabe kugwiritsidwa ntchito n’cholinga cholanda anthu ufulu woyankhula . . . komanso ufulu wopembedza, pofuna kulimbana ndi magulu ena koma makamaka a Mboni za Yehova.” *

Chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi chodziwika bwino ndipo chili m’mayiko osiyanasiyana. Iwo ali ndi ufulu wopembedza m’mayiko onse amene muli ulamuliro wa zipani zambiri komanso m’mayiko amene ndi mamembala a bungwe la European Union. Koma m’dziko la Russia a Mboni alibe ufulu umenewu. Ntchito ya boma la Russia yolimbana ndi a Mboni yakhala ikukula pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana ndipo izi zinayamba m’zaka za m’ma 1990. Ntchitoyi inakula mwadzidzidzi pamene dzikoli linakhazikitsa lamulo lolimbana ndi zinthu zoopsa ndipo linayamba kugwiritsa ntchito molakwika lamuloli ngati chida choponderezera a Mboni.

Kusamveka Bwino kwa Tanthauzo la Zinthu Zoopsa Kukuchititsa Kuti Lamulo Lizigwiritsidwa Ntchito Molakwa

Mu 2002, boma la Russia linakhazikitsa Lamulo Lolimbana ndi Zinthu Zoopsa monga njira yothana ndi za uchifwamba. Komabe, kusamveka bwino kwa tanthauzo la zinthu zoopsa kunabweretsa nkhawa yoti akuluakulu a boma akhoza kumagwiritsa ntchito lamuloli molakwika ndi cholinga chofuna kupondereza anthu. Mu 2003, Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu ya Bungwe la United Nations inalimbikitsa boma la Russia kuti lisinthe lamuloli komanso kuti lifotokoze momveka bwino tanthauzo la zinthu zoopsa, n’cholinga “chothetsa mchitidwe uliwonse wogwiritsa ntchito lamuloli molakwa.” *

Koma m’malo momveketsa lamuloli, kulisintha kumene kunachitika kunachititsa kuti lizigwiritsidwa ntchito m’njira zinanso zosiyanasiyana. Pamsonkhano wa Nduna za Bungwe la Mayiko a ku Ulaya wa mu 2012, anapeza mfundo yakuti: “Mu lamulo loyambirira, tanthauzo la zinthu zoopsa mbali ina linkanena kuti ndi ‘kuyambitsa mkangano chifukwa chosiyana mtundu, zipembedzo, ndale ndi zina zotero, ndipo kwachititsa ziwawa kapena kukanachititsa ziwawa.’ Lamuloli atalikonzanso mu 2006, anachotsamo mawu akuti ‘kwachititsa ziwawa kapena kukanachititsa ziwawa.’ . . . Choncho, chifukwa chakuti tanthauzo la mawu akuti ‘zinthu zoopsa’ silimveka bwino, mabungwe amene amaonetsetsa kuti anthu akutsatira malamulo, amagwiritsa ntchito lamuloli molakwa.”

Zimene anthu ankaganiza zoti akuluakulu a boma azigwiritsa ntchito lamuloli molakwa, zinalidi zoona. Izi zili choncho chifukwa chakuti mu 2007, Ofesi ya Mkulu Woimira Boma pa Milandu inapezerapo mwayi pa mmene mawu a m’lamuloli analembedwera ndipo analamula kuti a Mboni za Yehova afufuzidwe. Wachiwiri kwa Mkulu Woimira Boma pa Milandu a V. Ya. Grin, yemwenso anasayina kalata yaposachedwapa yochenjeza kuti atseka likulu la a Mboni, anapereka kalata kwa oimira boma pa milandu ena yowalamula kuti ayambe kufufuza a Mboni za Yehova. Kalatayo inali chizindikiro choyamba chosonyeza kuti ntchito yolimbana ndi a Mboni ichitika m’dziko lonselo komanso kuti boma ndi limene likukonza ntchitoyo.

Ngakhale kuti a Mboni sachita chilichonse chophwanya malamulo, gulu lalikulu la oimira boma pa milandu m’dziko la Russia lakhala likufufuza a Mboni maulendo oposa 500 kuyambira mu 2007. Lipoti la Msonkhano wa Nduna za Bungwe la Mayiko a ku Ulaya linanenanso kuti: “Lamulo Lolimbana ndi Zinthu Zoopsa limene linayamba kugwira ntchito mu 2002, lakhala likugwiritsidwa ntchito molakwika polimbana ndi zipembedzo zina, makamaka a Mboni za Yehova omwe alipo 162,000 m’dziko la Russia. Kugwiritsa ntchito lamuloli molakwa kwakula kwambiri kungoyambira pamene linasinthidwa mu 2006.” *

Lipoti la Msonkhano wa Nduna za Bungwe la Mayiko a ku Ulaya linati, “Lamulo la boma la Russia lolimbana ndi zinthu zoopsa lakhala likugwiritsidwa ntchito molakwika polimbana ndi zipembedzo zina, makamaka a Mboni za Yehova.”

Kuletsa Mabuku a Mboni Kwachititsa Kuti Iwo Aziponderezedwanso Kwambiri

Asanayambe kuganiza zoti atseke likulu la a Mboni lomwe lili pafupi ndi mzinda wa St. Petersburg, akuluakulu a boma ankangolimbana ndi mabuku a Mboni za Yehova. Oimira boma pa milandu ku Taganrog ndi ku Gorno-Altaysk analemba zisamani ku khoti, zonena kuti mabuku ambiri a Mboni aziwaona kuti ndi “oopsa” komanso kuti aikidwe pa mndandanda wa zinthu zomwe dzikolo limati ndi zoopsa.

Poyendera zimene anthu ena omwe amawatcha kuti ndi akatswiri anapeza, makhoti a ku Taganrog komanso ku Gorno-Altaysk anagamula nkhaniyo mokomera boma. Izi zinachitika mu 2009 ndi mu 2010 ndipo kuchokera nthawi imeneyo, zigamulo ziwirizi zachititsa kuti mabuku a Mboni okwana 52 aletsedwe ndipo zikupangitsa kuti a Mboni azinamiziridwa zinthu zambirimbiri. Akuluakulu enanso a boma m’zigawo zina za dzikoli akutsanzira zimene zinachitika ku Taganrog ndi ku Gorno-Altaysk. Pofika pano, makhoti alamula kuti mabuku okwana 87 a Mboni aikidwe pa mndandanda wa zinthu zimene ndi zoopsa.

A Mboni sakugwirizana ndi zimene makhoti anagamula ku Taganrog ndi ku Gorno-Altaysk komanso zimene makhoti ena onse ku Russia ananena zoti mabuku awo ndi oopsa. Iwo alembera Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya makalata okwana 28 ndi cholinga choti lichitepo kanthu pa zimene akuwanamizira zoti ndi gulu loopsa komanso nkhanza zina zimene akuwachitira. Khotili likuyembekezereka kupereka chigamulo chake pa nkhani zokwana 22 posachedwapa. Pamene linkadziteteza ku khotili, boma la Russia linavomereza kuti mabuku ambiri a Mboni amene ali pa mndandanda wa zinthu zoopsa “salimbikitsa anthu kuti azichita zachiwawa kapenanso zinthu zimene zingayambitse zachiwawa.”

Ufulu Woyankhula Ukuphwanyidwa

Akuluakulu a boma la Russia atakwanitsa cholinga chawo choti mabuku a Mboni akhale m’gulu la zinthu “zoopsa,” zinali ngati “mwalamulo” apatsidwa mphamvu zoti ayambe kulimbana ndi a Mboni komanso kupitiriza kuwalanda ufulu wochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo.

  • Mu 2010, akuluakulu a boma ku Russia analanda chilolezo kwa a Mboni choti azitha kulowetsa komanso kugawa magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’dzikolo. Magazini awiriwa ndi amene amasindikizidwa kwambiri pa dziko lonse lapansi. Magazini ya Nsanja ya Olonda yakhala ikusindikizidwa kuyambira mu 1879.

  • Kuyambira mu March 2015, akuluakulu a boma la Russia akhala akukana kuti mabuku a Mboni za Yehova azilowa m’dzikolo.

  • Kuyambira mu July 2015, webusaiti ya Mboni ya jw.org yakhala yoletsedwa ku Russia ndipo zimenezi zachititsa kuti anthu asakhale ndi mwayi wopeza mabuku a Mboni pa zipangizo zawo zamakono. Kulimbikitsa anthu kuti azigwiritsa ntchito webusaitiyi ndi mlandu m’dzikoli.

  • Chakumayambiriro kwa chaka cha 2016, woimira boma pa milandu ku Vyborg analemba chisamani chonena kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe limafalitsidwa ndi a Mboni, likhale m’gulu la “zinthu zoopsa.”

Kuonjezera pa kuwaphwanyira ufulu wawo wolankhula, akuluakulu a boma la Russia akhala akugwiritsa ntchito mabuku omwe ali pa mndandanda wa zinthu zoopsa ngati chifukwa chowachititsa kuyambanso kufufuza mabungwe amene amaimira a Mboni komanso kuzenga milandu wa Mboni aliyense amene am’peza akuchita zinthu zokhudza chipembedzochi.

Zimene Zimachitika Akamafufuza Zinthu Komanso Kuchititsa a Mboni Kuoneka Olakwa

Buku lililonse akaliyika pa mndandanda wa zinthu zimene ndi zoopsa, amaletsa kuligawa kwa anthu, kulisindikiza kapena kulisunga ndi cholinga choti lidzagawidwe m’tsogolo. Izi zachititsa kuti akuluakulu a boma m’madera osiyanasiyana apezerapo mwayi womakatenga chilolezo ku khoti kuti akachite chipikisheni m’nyumba za a Mboni komanso mu Nyumba za Ufumu kuti apeze mabuku omwe ndi oletsedwa.

Nthawi zambiri amachita chipikishenicho mwankhanza ndipo amalanda zinthu zina zimene mwalamulo sakuyenera kulanda monga katundu komanso mabuku onse, kaya mabukuwo ali pa mndandanda wa zinthu zoopsa kapena ayi.

  • Mu August 2010, m’dera la Yoshkar-Ola, gulu la apolisi komanso asilikali pafupifupi 30 anasokoneza a Mboni pa nthawi imene ankapemphera. Apolisiwo anafufuza pa malowo ndipo anagwira ena mwa a Mboniwo n’kuwapotokolera manja kumbuyo, kuwalanda zinthu, zikalata komanso mabuku awo.

  • Mu July 2012, apolisi m’dziko la Karelia omwe anali ndi mfuti zoopsa kwambiri ndipo anavala zipewa zobisa nkhope, anachitira nkhanza wa Mboni wina pa gulu la anthu. Iwo anamenyetsa nkhope ya wa Mboniyo kutsogolo kwa galimoto yake n’kupindira manja ake kumsana kwake. Komanso apolisiwo anachita chipikisheni m’nyumba zambiri za a Mboni n’kuwalanda katundu komanso mabuku awo, kaya mabukuwo anali pa mndandanda wa zinthu zoopsa kapena ayi.

  • Mu March 2016, apolisi m’dziko la Tatarstan analowa mu Nyumba ya Ufumu komanso m’nyumba za a Mboni n’kutengamo zinthu zosiyanasiyana. Anatenga zinthu monga makompyuta, matabuleti komanso mabuku.

Anajambulidwa pa vidiyo akuika “umboni”

Akuluakulu a boma anafika mpaka pojambula mavidiyo achinsinsi oonetsa a Mboni ali m’nyumba zawo komanso m’Nyumba za Ufumu. Iwo afika mpaka polumikiza zinthu zina ku mafoni a a Mboni ndi cholinga choti azimvetsera zimene akukambirana, kuwerenga mauthenga a pakompyuta omwe a Mboni amatumizirana komanso kupeza uthenga pogwiritsa ntchito njira zolakwika. Apolisi ena afika pomaika mabuku omwe ndi oletsedwa mu Nyumba za Ufumu ndi cholinga choti akhale ndi umboni woti akagwiritse ntchito kukhoti. A Mboni ambiri azengedwa milandu chifukwa cha zinthu ngati zimenezi.

Kuthetsedwa kwa Mabungwe a Mboni Kwabweretsa Milandu Yambiri

Kuonjezera pa kuzenga milandu a Mboni, akuluakulu a boma amagwiritsa ntchito mabuku amene akuluakuluwo amakaika mu Nyumba za Ufumu ngati “umboni” ndi cholinga chofuna kuthetsa mipingo yosiyanasiyana ya Mboni m’dzikoli. * Gulu lililonse lachipembedzo akalithetsa pa chifukwa choliganizira kuti ndi “loopsa,” boma limalanda china chilichonse chimene gululo linali nacho. Zimenezi zachititsa kuti a Mboni asakhale ndi malo opemphereramo ndipo ndi zimenenso zinachitika ku Taganrog ndi ku Samara. Akuluakulu a boma m’mizinda ina akuchitanso zofanana ndi zimenezi.

A Mboni za Yehova akuzengedwa mlandu ku Taganrog m’dziko la Russia

Akuluakulu a boma atatseka mpingo wa Mboni wa ku Taganrog, anachita zinthu zosemphana ndi malamulo ponena kuti a Mboni akasonkhana kuti apemphere, amakhala kuti “akupitiriza kuchita zinthu zosemphana ndi malamalo chifukwa gululi ndi loletsedwa.” Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, akuluakulu a boma ku Taganrog ananena kuti a Mboni ena 16 ndi olakwa chifukwa chosonkhana pamodzi n’kuchita mapemphero awo omwe sankasokoneza aliyense. Kusonkhana malo amodzi n’kuchita mapemphero kotereku n’kumene a Mboni za Yehova amachita pa dziko lonse lapansi. Kwa nthawi yoyamba kuchokera pamene ulamuliro wa Soviet Union unatha, panopa ku Taganrog umakhala mlandu a Mboni za Yehova akasonkhana n’kumapemphera.

Kutseka Maofesi a Mboni Kumene Akufuna Kuchita Kukusonyeza Kuti Zinthu Zafika Poipa Kwambiri

Likulu la Mboni za Yehova ku Russia

Ngati boma lingathetse likulu la Mboni za Yehova ku Russia, zikutanthauza kuti likululi adzalitseka komanso kuletsa ntchito ina iliyonse imene likululi limachita. Zingachititsenso kuti a Mboni m’dzikoli aziimbidwa mlandu chifukwa chochita misonkhano yawo komanso kuuza anthu ena zimene amakhulupirira, ngati mmene zilili ku Taganrog. Zingapangitse kuti iwo akhale ndi ufulu wokhulupirira zimene akufuna koma osakhala ndi ufulu wochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo ndi anthu ena. *

Bambo Philip Brumley, omwe amaimira Mboni za Yehova pa nkhani za malamulo ku New York, ananena kuti: “Kuika a Mboni za Yehova m’gulu la magulu oopsa komanso kuika mabuku awo pa mndandanda wa zinthu za magulu a za uchifwamba, ndi kusatsatira malamulo komanso kupanda chilungamo. Akuluakulu a boma la Russia akugwiritsa ntchito lamuloli m’njira yosemphana ndi malamulo oyendetsera dziko lawo, malamulo amene mayiko ambiri amayendera, mfundo zimene mayiko a m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya amatsatira, komanso mosemphana ndi Chikalata cha Mfundo za Ufulu Wachibadwidwe cha Bungwe la United Nations. Akugwiritsa ntchito lamuloli n’cholinga chopondereza a Mboni kuti asamachite zinthu zokhudza kulambira mwamtendere komanso kulimbana ndi likulu lawo lomwe ndi phata la ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo.”

Bambo Vasiliy Kalin, omwe ndi oimira likulu la Mboni za Yehova m’dziko la Russia, anati: “A Mboni za Yehova m’dziko la Russia akhala akuchita zinthu zokhudza chipembedzo chawo kuyambira zaka za m’ma 1900 ndipo anapirira pamene ankazunzidwa kwambiri panthawi yaulamuliro wa Soviet Union. Kenako ulamuliro utasintha, ankangodziwika monga anthu amene ankaponderezedwa. Tikufuna kupitiriza kuchita zinthu zokhudza chipembedzo chathu mwaufulu kuno ku Russia. Zinthu zabodza zimene amatineneza kuti ndife gulu loopsa, cholinga chake ndi kungofuna kutsekereza mfundo yoti pali anthu ena amene safuna chipembedzo chathu chifukwa chakuti sagwirizana ndi zimene timakhulupirira. Si ife gulu loopsa.”

A Mboni za Yehova akukhulupirira kuti dziko la Russia liteteza ufulu wawo wopembedza ngati mmene mayiko enanso ambiri akuchitira. Iwo akupemphanso kuti Ofesi ya Mkulu Woimira Boma pa Milandu isiye kulimbana ndi likulu lawo komanso kuti dziko la Russia lizilemekeza ufulu umene anthu azipembedzo zing’onozing’ono ali nawo. Funso ndi lakuti, Kodi dziko la Russia lichita zimenezi? Kapena kodi liyambiranso kupondereza a Mboni za Yehova ngati mmene linkachitira pa nthawi ya ulamuliro wa Soviet Union?

^ ndime 4 Zimene Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu ya Bungwe la United Nations inanena mu lipoti lake la nambala 7 lokhudza dziko la Russia. CCPR/C/RUS/CO/7, 28 April 2015, ndime 20.

^ ndime 7 Zimene Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu ya Bungwe la United Nations inanena zokhudza dziko la Russia komanso mfundo nambala 40 ya m’Pangano la Mayiko a Bungwe la UN yomwe imati dziko lililonse liyenera kupereka lipoti. CCPR/CO/79/RUS, December 1, 2003, ndime 20.

^ ndime 10 Zimene zili mu lipoti la Msonkhano wa Nduna za Bungwe la Mayiko a ku Ulaya la pa 14 September 2012, ndime 497 zonena kuti dziko la Russia liyenera kulemekeza zimene zili m’malamulo komanso zonse zimene dzikoli linalonjeza.

^ ndime 30 Ku Russia, zipembedzo zomwe zakwanitsa zinthu zina zimene a boma akufuna, zikhoza kupanga bungwe lowaimira m’dera laling’ono, monga m’tauni kapena mu mzinda. Koma mabungwe oterewa si amene amayendetsa ntchito zonse zimene chipembedzocho chimachita m’dzikolo. Kukhala ndi bungwe lowaimira kumathandiza chipembedzocho kuti chizitha kupanga zinthu zosiyanasiyana monga kuchita lendi kapena kugula malo.

^ ndime 33 Zimenezi zikusemphana ndi zimene zili mu Gawo 28 la malamulo oyendetsera dziko la Russia limene limati: “Munthu wina aliyense adzapatsidwa ufulu wotsatira chikumbumtima chake, ufulu wopembedza, kuphatikizapo ufulu wokhala m’chipembedzo china chake, kaya payekha kapena limodzi ndi anthu ena, kapenanso kusakhala m’chipembedzo chilichonse. Adzapatsidwanso ufulu wosankha, kusunga kapenanso kuuza ena zokhudza chipembedzo chake ngakhalenso kuchita zinthu za m’chipembedzocho.”

^ ndime 40 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania ndi bungwe limene limagwiritsidwa ntchito pothandiza pa ntchito zosiyanasiyana zimene a Mboni za Yehova amachita padziko lonse ndipo cholinga chake sikupanga phindu. Limeneli ndi bungwe limene lili ndi mphamvu pa mabuku onse a Mboni za Yehova.