Pitani ku nkhani yake

JUNE 28, 2016
RUSSIA

Khoti Likuyembekezeka Kupereka Chigamulo Chake pa Nkhani Yokhudza Kutseka Likulu la a Mboni M’dzikolo la Russia

Khoti Likuyembekezeka Kupereka Chigamulo Chake pa Nkhani Yokhudza Kutseka Likulu la a Mboni M’dzikolo la Russia

Posachedwapa khoti la m’chigawo cha Tver ku Moscow likuyembekezeka kupereka chigamulo chake pa nkhani imene a Mboni za Yehova anapanga apilo ku khotili. A Mboni anapanga apilo nkhani yokhudza kalata imene analemba a mu Ofesi ya Mkulu Woimira Boma Pamilandu yowopseza kuti atseka likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo. Kalatayo inanena kuti a Mboniwo amachita “zinthu zoopsa.”

A Mboni za Yehova akupempha zoti khotilo ligamule kuti zimene ananena woimira boma pa milanduyo ndi zosemphana ndi malamulo. Zimene boma likufuna kuchitazo ndi kusokoneza ufulu umene a Mboni ali nawo wochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo komanso kugwiritsa ntchito dala molakwa lamulo la m’dzikoli lolimbana ndi zinthu zoopsa.

Bambo Vasiliy Kalin, omwe ndi woyimira likulu la a Mboni m’dziko la Russia ananena kuti: “Sitinachitepo chinthu chilichonse choopsa ndipo tikukhulupirira kuti khoti lionetsetsa kuti chilungamo chachitika pa nkhani imeneyi.”