Pitani ku nkhani yake

Nyumba ya wa Mboni za Yehova yomwe anthu anawotcha ku Lutsino m’chigawo cha Moscow

16 JUNE, 2017
RUSSIA

A Mboni za Yehova Akuvutika Kwambiri Chifukwa cha Chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia

A Mboni za Yehova Akuvutika Kwambiri Chifukwa cha Chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia

Chigamulo chomwe Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linapereka pa 20 April 2017, chapangitsa kuti a Mboni za Yehova m’dziko lonse la Russia ayambe kuvutika. Akuluakulu a boma aphwanya ufulu wa a Mboniwa powaletsa kuchita chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chawo. Chigamulochi chachititsanso kuti nzika zina za m’dzikoli zipezerepo mwayi wochitira nkhanza a Mboni.

Boma la Russia Likupondereza Ufulu wa Anthu

Dennis Christensen

Milandu Yomwe a Mboni za Yehova Akuzengedwa

 • Pa 25 May, apolisi anakasokoneza misonkhano yachipembedzo ya Mboni za Yehova kumpingo wa ku Oryol. Pa nthawiyi apolisi anamanga a Dennis Christensen. A Christensen ndi nzika ya ku Denmark ndipo ndi mkulu mumpingo wa ku Oryol. Iwo akuwasunga kundende podikira kuzengedwa kwa mlandu wawo pa 23 July. Oimira boma pa milandu akuyembekezeka kudzazenga a Christensen mlandu wofuna “kuchita zinthu zofuna kuyambitsa chisokonezo.” Ngati angadzawapeze olakwa, akhoza kudzawagamula kuti akhale kundende kwa zaka 6 kapena 10.

Boma Linatumiza Mauthenga Ochenjeza Mipingo ya Mboni za Yehova

 • Pa 4 May, oimira boma pa milandu anatumiza kalata yochenjeza kwa tcheyamani wa mpingo wa ku Krymsk. Kalatayo inachenjeza kuti tcheyamaniyo kapena munthu wina aliyense amene angachititse msonkhano wachipembedzo adzaimbidwa mlandu.

 • Kuchokera pomwe Khoti Lalikulu Kwambiri linapereka chigamulo chake, mipingo pafupifupi 5 inalandira makalata ochenjezawa.

Apolisi Anasokoneza Misonkhano

 • Pa 22 April, apolisi anakalowa m’nyumba ina momwe munkachitikira msonkhano wachipembedzo ku Dzhankoy m’chigawo cha Crimea. Apolisiwa analowa m’nyumbayi msonkhanowu utatsala pang’ono kutha. Iwo ananena kuti kungochokera pomwe Khoti Lalikulu Kwambiri linapereka chigamulo chake, a Mboni alibenso ufulu wopanga msonkhano wachipembedzo. Anafufuzafufuza zinthu m’nyumba yonseyo kenako n’kuitseka kuti musadzachitikirenso misonkhano yachipembedzo.

 • Kuchokera nthawi yomwe Khoti Lalikulu Kwambiri linagamula mlandu wa Mboni za Yehova, misonkhano ya m’malo 5 inasokonezedwa ndi apolisi. Pamisonkhano imeneyi, umodzi unkachitikira m’nyumba ya munthu.

“Ndakhumudwa kwambiri ndi kuzunzidwa kwa Mboni za Yehova ku Russia. A Mboni za Yehova amachita zinthu zawo mwamtendere. Ndikupempha akuluakulu a boma la Russia kuti aonetsetse kuti akulemekeza ufulu wa anthu pa nkhani ya chipembedzo, zimene munthu amakhulupirira, ufulu wofotokoza maganizo ako komanso ufulu woti a Mboni za Yehova azichita misonkhano yawo mwamtendere. Zimenezi ndi zogwirizana ndi lamulo lokhudza ufulu wa anthu lomwe mayiko onse anasainira komanso zomwe zili m’chikalata cha Bungwe Loona za Chitetezo Komanso Mgwirizano wa Mayiko a ku Europe.]”—Michael Georg Link, Mkulu wa bungwe Loona za Chitetezo ku Mayiko a ku Europe lomwe lili pansi pa Ofesi Yoona za Ulamuliro wa Zipani Zambiri ndi Ufulu wa Anthu.

Ana Asukulu a Mboni Akuvutika

 • Pa 24 April, m’mudzi wa Bezvodnoye m’chigawo cha Kirov, mphunzitsi wina ananyoza ana awiri asukulu omwe mayi awo ndi a Mboni za Yehova. Mphunzitsiyu akuti anachita zimenezi chifukwa a Mboni analetsedwa ku Russia.

 • Pa 17 May, mphunzitsi wamkulu pasukulu ina mumzinda wa Moscow, analemba kalata yochenjeza makolo a mwana wina wa zaka 8. Mwanayu ankauza mnzake wa m’kalasi zokhudza Mulungu. M’kalatayo, mphunzitsiyo analembamo za chigamulo chomwe Khoti Lalikulu Kwambiri linanena. Choncho mphunzitsiyu ananena kuti n’zosavomerezeka kuti ana akakhala kusukulu azikambirana nkhani zosagwirizana ndi maphunziro. Mphunzitsi wamkuluyo anaopseza kuti akasuma nkhaniyo kupolisi komanso kuti mwanayo amusamutsa pasukulupo.

A Mboni Ena Anakanizidwa Mwayi Wogwira Ntchito Zina M’malo mwa Usilikali

 • Pa 28 April, bungwe la asilikali lolemba anthu ntchito la ku Cheboksary ndi ku Marposadskiy linakana kalata ya wa Mboni wina yopempha kuti azigwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Bungweli linanena kuti a Mboni za Yehova amachita zinthu zosokoneza ndipo sangapatsidwe mwayi wogwira ntchito zina.

 • Bungweli linakanira anthu enanso awiri a Mboni za Yehova atapempha kuti awapatse mwayi wogwira ntchito zina m’malo mwa usilikali.

Woimira Mboni za Yehova pa nkhani za malamulo, a Philip Brumley ananena kuti zimene boma likuchita ndi zotsutsana. Iwo anati: “Boma likukana kupereka mwayi wogwira ntchito zina kwa anyamata a Mboni powaganizira kuti amachita zauchigawenga. Koma a boma omwewonso akufuna kuti anyamata omwe akuwaona ngati zigawengawa azikagwira ntchito za usilikali. Ndiye kodi n’zomveka kuti boma lingalole zigawenga kuti zikhale m’gulu la asilikali ake?”

A Mboni Akusalidwa Komanso Kuchitiridwa Nkhanza Ndi Anthu A M’dera Lawo

Anthu Ena Akuchitira a Mboni za Yehova Zinthu Zachiwawa

 • Pa 30 April, ku Lutsino m’chigawo cha Moscow, munthu wina anawotcha nyumba ya banja lina la Mboni komanso nyumba ya makolo awo omwe ndi achikulire. Munthuyo asanawotche nyumbazi ankasonyeza kuti amadana ndi chipembedzo cha banjali.

 • Pa 24 May, ku Zheshart, m’chigawo cha Komi, anthu achiwawa anawononga nyumba imene a Mboni za Yehova amachitira misonkhano yawo.

  Nyumba ya Ufumu ya ku Zheshart yomwe inawonongedwa ndi anthu achiwawa

 • Kuchokera pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linapereka chigamulo chake pa 20 April 2017, anthu anawononga nyumba 9 zimene a Mboni ankachitira misonkhano yawo.

 • Pa 26 April, wa Mboni wina ankachoka pakhomo pake ku Belgorod, ndipo munthu wina anakuwa kuti “chipembedzo chanu chinatsekedwa,” kenako munthuyo anamenya wa Mboniyo.

 • Pa 11 May, gulu la anthu linasokoneza misonkhano ya Mboni za Yehova ku Tyumen. Anthuwa ankatukwana komanso kunyoza a Mboniwo ndipo anawaopseza kuti awakhaulitsa.

A Mboni Ena Anachotsedwa Ntchito

 • Pa 15 May, akuluakulu a kampani ina yopanga mankhwala ku Dorogobuzh, m’dera la Smolensk anachotsa ntchito anthu onse amene anali a Mboni za Yehova. Akuluakuluwo ananena kuti asilikali a boma anawalamula kuti achotse ntchito a Mboni onse chifukwa chakuti ndi anthu oyambitsa chisokonezo ndipo sakuyenera kugwira ntchito pakampaniyo.

 • Kuchokera pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linapereka chigamulo chake, makampani enanso atatu akhala akuopseza a Mboni kuti awachotsa ntchito chifukwa chakuti ali m’chipembedzo choyambitsa chisokonezo. Ku Yashkino m’dera la Kemerovo, apolisi anakakamiza wa Mboni wina kuti aulule zokhudza a Mboni anzake, koma munthuyo anakana. Apolisiwo ananena kuti kukhala m’chipembedzo chomwe boma linaletsa ndi mlandu ndipo anati a Mboni za Yehova amachita zinthu ngati gulu la zigawenga la ISIS.

A Mboni za Yehova ndi Okhudzidwa ndi Zimene Zikuchitikira Anzawo ku Russia

Zaka 10 zapitazo kudzafika pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linapereka chigamulo chake, a boma akhala akuphwanya ufulu wachipembedzo wa Mboni za Yehova ku Russia. Zimenezi zinachititsa kuti azizunzidwa komanso kuchitiridwa nkhanza kwambiri. Ndiye pambuyo pa chigamulo cha khoti chija, n’zokayikitsa ngati a Mboniwo angakhale motetezeka. Zimene zikuchitikazi zikusonyeza kuti chigamulocho chinapangitsa kuti anthu ambiri azidana ndi a Mboni ndipo chapereka mphamvu kwa anthu komanso akuluakulu a boma kuti aziwachitira nkhanza. A Mboni za Yehova padziko lonse ndi okhudzidwa kwambiri ndi zimene zingachitikire a Mboni anzawo ku Russia ngati Khoti la Apilo lingagwirizane ndi chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri akamadzazenganso mlanduwu pa 17 July, 2017.

A Brumley ananena kuti: “Palibe amene wapereka umboni womveka kuti a Mboni za Yehova amachita zinthu zosokoneza. Zinthu zoopsa zimene akuganizira kuti a Mboni amachita sizikupereka chifukwa chomveka choti aziwazunzira. Boma la Russia likuyenera kuganiziranso zimene likuchitira a Mboni za Yehova mogwirizana ndi zimene malamulo oyendetsera dziko lawo amanena komanso potengera mfundo za mumgwirizano umene mayiko anasainirana pa nkhani yokhudza ufulu wa chipembedzo.”