Pitani ku nkhani yake

17 FEBRUARY, 2017
RUSSIA

Khoti Lalikulu Kwambiri Russia Lalamula Kuti Bungwe Linanso la Mboni za Yehova Lithetsedwe Chifukwa Limachita Zinthu Zoopsa

Khoti Lalikulu Kwambiri Russia Lalamula Kuti Bungwe Linanso la Mboni za Yehova Lithetsedwe Chifukwa Limachita Zinthu Zoopsa

Pa 9 February, 2017, khoti lalikulu kwambiri ku Russia linagamula kuti bungwe la Mboni za Yehova la ku Birobidzhan lithetsedwe. Khotili linachita zimenezi pogwirizana ndi zimene khoti lina laling’ono linagamula zoti bungwe la Mbonilo limachita zinthu zoopsa ndipo linalamula bungwelo kuti lisiye kuchita chilichonse chokhudza chipembedzo chawo.

Chigamulochi chinaperekedwa pogwiritsa ntchito umboni wabodza. Mu February 2015 ndi mu January 2016, apolisi anaika mabuku oletsedwa m’malo amene a Mboni anapanga lendi kuti azichitiramo misonkhano yawo. Kenako apolisiwo anakapanga chipikisheni m’malowo n’kunena kuti a Mboni apezeka ndi mabuku oletsedwa. M’mwezi wa January, apolisi omwe anavala zinthu zobisa nkhope anasokoneza msonkhano wa a Mboni ndiponso anaika mabuku oletsedwa pansi pa mpando a Mboniwo akuona.

Khoti la mumzinda wa Moscow linanena kuti zimene mkulu woimira boma pamilandu ananena zoti akufuna kutseka likulu la a Mboni ku Russia zikhoza kuyamba kugwira ntchito. Atanena zimenezi, bungwe la Mboni za Yehova la ku Birobidzhan, lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda ku Russia, ndi limene linali loyamba kuthetsedwa.