Pitani ku nkhani yake

MAY 31, 2018
RUSSIA

Wa Mboni Winanso ku Russia Akuimbidwa Mlandu Wochita Zinthu Zoopsa

Wa Mboni Winanso ku Russia Akuimbidwa Mlandu Wochita Zinthu Zoopsa

Bambo Arkadya Akopyan omwe ndi a Mboni za Yehova, akhala akuimbidwa mlandu kwa chaka chimodzi tsopano powaganizira kuti anachita zinthu zoopsa. Iwo ali ndi zaka 70 ndipo anapuma pantchito ya utelala. Ngati angapezeke olakwa, bambowa alipiritsidwa chindapusa cha ndalama zambiri kapena akakhala m’ndende mpaka zaka 4.

Bambo Akopyan akuwaganizira kuti “ankalimbikitsa anthu kudana ndi anthu azipembedzo zina” chifukwa cha nkhani yomwe anakamba ku Nyumba ya Ufumu yomwe akhala akusonkhanako kwa zaka zambiri. Pamene ankawazenga mlandu, woimira boma pa milandu anadalira kwambiri maumboni omwe anaperekedwa ndi anthu 6 omwe si a Mboni za Yehova. Anthuwo ananena kuti pa nthawi yomwe bambo Akopyan ankakamba nkhani yawo, analankhula zinthu zonyoza komanso anawapatsa mabuku “oopsa” kuti akagawirenso anthu ena.

Bambo Akopyan komanso anthu ena amene amawadziwa bwino bambowa, anakana zoti analankhula zinthu zonyoza ndiponso kugawa mabuku “oopsa.” Popereka umboni wake m’khotimo, loya wa bambo Akopyan ananena kuti anthu 6 omwe anapereka umboni m’khotimo, sanali pafupi ndi Nyumba ya Ufumu yomwe akuti bambo Akopyan ananeneramo zinthu zonyozazo. Kuonjezera pamenepo, a Mboni sapereka mabuku awo kwa anthu amene si a Mboni kuti anthuwo akawagawirenso kwa anthu ena. A Sonya omwe ndi akazi awo a bambo Akopyan, si a Mboni za Yehova ndipo anauza a khoti pa nthawi yomwe ankawafunsa mafunso kuti akhala m’banja mosangalala ndi bambo Akopyan kwa zaka 40 koma amuna awo sanakakamizepo wachibale wawo kapena wa amuna awowo kuti akhale wa Mboni za Yehova.

Woweruza wina dzina lake Oleg Golovashko analamula kuti pachitike kafukufuku n’cholinga choti adziwe ngati zimene bambo Akopyan analankhula pokamba nkhani yawo zinalidi ‘zolimbikitsa anthu kudana ndi anthu azipembedzo zina.’ Posachedwapa, pamene woweruza milandu ankamvetsera mlandu wa bambo Akopyan pa 15 May, 2018, ananena kuti apitiriza kuzenga mlanduwu koma ananenanso kuti kafukufukuyo ayenera kutha pofika m’mwezi wa September 2018. Mlanduwu adzaumvetseranso pa 5 June ndipo pa tsikuli bambo Akopyan adzafunsidwa mafunso. Kuyambira pamene Khoti la M’Boma la Prokhladny linayamba kuzenga mlandu wa bambo Akopyan mu May 2017, bambowa analetsedwa kuchoka m’dera limene amakhala ngakhale kuti panopa sakusungidwa m’ndende.

A Gregory Allen omwe ndi wachiwiri kwa loya wa Mboni za Yehova, anati: “Bambo Akopyan ndi mmodzi mwa anthu omwe akuzunzidwa chifukwa cha zimene boma la Russia likuchita pogwiritsa ntchito molakwika lamulo loletsa zinthu zoopsa ponamizira a Mboni za Yehova kuti amachita zinthu zoopsa. Bambowa ndi osalakwa, amamvera malamulo a boma ndipo cholinga chawo n’choti azipembedza Mulungu mwamtendere. Zimene boma la Russia likuchita polimbana ndi a Mboni za Yehova zikuika moyo wa a Mboni pa chiopsezo komanso zikusokoneza mgwirizano wa zikhalidwe zosiyanasiyana za m’dzikolo.”

Bambo Akopyan ndi wa Mboni wachiwiri amene akuimbidwa mlandu mopanda chilungamo “wochita zinthu zoopsa.” A Dennis Christensen omwenso ndi a Mboni ndipo amakhala ku Oryol, anayamba kuimbidwa mlandu mu February 2018. Iwo akhala akusungidwa m’ndende popanda kuwazenga mlandu kwa chaka chimodzi, ndipo ngati atawapeza olakwa akhoza kugamulidwa kuti akhale m’ndende mpaka zaka 10. * A Mboni enanso 7 m’madera osiyanasiyana ku Russia akusungidwa m’ndende koma milandu yawo sinazengedwe.

^ ndime 7 A Mboni awiri onsewa anaimbidwa mlandu potengera zomwe zili m’magawo osiyana a m’Buku la Zamalamulo a Zaupandu. Bambo Akopyan akuganiziridwa kuti anapalamula mlandu wolimbikitsa anthu kudana ndi anthu azipembedzo zina zomwe n’zosemphana ndi Gawo 282(1). A Dennis Christensen akuwaganizira kuti anapalamula mlandu wotsogolera ntchito za chipembedzo chomwe chagamulidwa kuti ndi choopsa zomwe n’zosemphana ndi Gawo 282.2(1). Munthu amene wapalamula mlandu umenewu amapatsidwa chilango chokhwima.