Pa 12 October, 2016, khoti la m’chigawo cha Tverskoy ku Moscow linakana apilo yomwe a Mboni anapereka. A Mboni anaona kuti kalata yomwe Woimira Boma pa Milandu analemba yoopseza kuti atseka likulu lawo lomwe lili pafupi ndi mzinda wa St. Petersburg, ndi yosemphana ndi malamulo. Kalatayi inalembedwa pa 2 March 2016 ndipo inafotokoza kuti alibe vuto ndi likulu la Mbonilo, koma akulimbana ndi mipingo ina ya Mboni imene akuti imachita “zinthu zobweretsa chisokonezo.” Koma popeza kuti likululi ndi limene limayang’anira mipingo yonse ya Mboni m’dziko la Russia, liyenera kuyankha mlandu. Akuluakulu a boma a m’madera osiyanasiyana anagwiritsa ntchito maumboni komanso nkhani zabodza poimba mlandu a Mboni kuti amachita “zinthu monyanyira” komanso “zosemphana ndi malamulo.” Woweruza mlandu anakana kuti a Mboniwo afotokoze mbali yawo kapena kuonetsa mavidiyo osonyeza apolisi akuika mabuku omwe amati ndi oopsawo m’malo olambirira a Mboni za Yehova.

A Mboniwo apanganso apilo za nkhaniyi kukhoti la mumzinda wa Moscow. Ngati khotili lingagamule kuti a Mboniwo ndi olakwa, ndiye kuti zimene Mkulu Woimira Boma pa Milandu ananena, ziyamba kugwira ntchito. Chigamulochi chidzachititsa kuti a Mboni za Yehova asakhalenso ndi ufulu wolambira m’dziko lonselo. Ngati khotilo lingagamuledi kuti a Mboni za Yehova ndi olakwa, komanso chifukwa cha umboni wabodza womwe apolisi akupereka woti a Mboni ndi kagulu koopsa, Woimira Boma pa Milandu akhoza kuyamba kuchita zinthu zoti likulu la Mbonilo litsekedwe.