Khoti la mumzinda wa Moscow lakonza zodzamvetsera apilo ya Mboni za Yehova ponena za chenjezo lochokera ku boma lomwe likulu lawo lapatsidwa. Pa 16 January, 2017 nthawi ya 11:10 m’mawa, khotili lidzamvetsera apiloyi ndipo mwina lidzapekerekeratu chigamulo chake tsiku lomwelo.

A Mboni akufuna kutsimikizira boma kuti milandu yomwe akuwaimba yoti chipembedzo chawo ndi “kagulu koopsa,” ndi yabodza ndipo ilibe umboni. Milandu yabodzayi yangopekedwa ndi akuluakulu a boma pofuna kusonyeza kuti zinthu zachipembedzo zomwe a Mboniwa amachita mwamtendere, ndi zosemphana ndi malamulo. Pa 12 October, 2016 woweruza milandu m’khoti la Tverskoy mumzinda wa Moscow a M. S. Moskalenko, anakana kumvetsera umboni komanso kuonera vidiyo yomwe inasonyeza zinthu zosemphana ndi malamulo zomwe akuluakulu a boma komanso apolisi anachitira a Mboni.

Loya woona za ufulu wa anthu m’mayiko osiyanasiyana a James Andrik ananena kuti: “Chigamulo chomwe chingaperekedwe chikhala ndi zotsatirapo zazikulu. Ngati khoti la mumzinda wa Moscow lingakane apiloyo, a mu ofesi yozenga milandu adzafuna kuonetsa mphamvu zawo pa chiopsezo chomwe anapereka kulikulu la Mboni. A mu ofesiyi akhoza kutseka likululo komanso kuchitira nkhanza a Mboni onse komanso kuletsa kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chisapezekenso m’dziko lonse la Russia. Koma ngati khotilo lingachite zinthu mogwirizana ndi apiloyo, ndiye kuti chilungamo chioneka.”