Pitani ku nkhani yake

JULY 14, 2016
RUSSIA

Khoti Lina Liyamba Kumva Mlandu Umene a Mboni Achita Apilo pa Nkhani Yofuna Kutseka Likulu Lawo ku Russia

Khoti Lina Liyamba Kumva Mlandu Umene a Mboni Achita Apilo pa Nkhani Yofuna Kutseka Likulu Lawo ku Russia

Khoti la m’chigawo cha Tver ku Moscow lavomera apilo yomwe a Mboni anachita pa nkhani yokhudza kalata imene a mu Ofesi ya Mkulu Woimira Boma pa Milandu ku Russia analemba, yowopseza kuti atseka likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo. Khotilo lidzazenga mlanduwu pa 18 July, 2016, ndipo likuyembekezeka kunena ngati zimene boma la Russia likufuna kuchitazi zili zogwirizana ndi malamulo kapena ayi.

Popitiriza kulimbana ndi a Mboni za Yehova, akuluakulu oyang’anira dera lina la Arkhangelsk ku Russia anakapereka chisamani kwa bambo Aleksandr Konovalov omwe ndi Nduna Yoona Za Chilungamo m’dzikolo. Mu chisamanicho, akuluakuluwo anakakamiza boma kuti likhazikitse lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo komanso kuthetsa mabungwe onse omwe amaimira a Mboniwo pa nkhani zosiyanasiyana.