Pitani ku nkhani yake

Apolisi akuthyola nyumba yomwe a Mboni akuchitiramo msonkhano ku Tomsk

JUNE 20, 2018
RUSSIA

A Mboni Enanso ku Russia Anamangidwa Apolisi Atathyola Nyumba Zawo

A Mboni Enanso ku Russia Anamangidwa Apolisi Atathyola Nyumba Zawo

M’mwezi wapitawu, akuluakulu a boma la Russia akhala akuchitira a Mboni za Yehova enanso zinthu zankhanza, kuwamanga, komanso kuwaika m’ndende ponamizira kuti akufuna kuthana ndi anthu ochita zinthu zoopsa. Apolisi ankalowa m’nyumba za a Mboni ku Birobidzhan, Khabarovsk, Magadan, Orenburg, Naberezhnye Chelny, Perm, Pskov, Saratov, komanso ku Tomsk. Iwo anamanga azibambo 15 a Mboni ndipo chiwerengero cha amene akusungidwa m’ndende popanda kuwazenga mlandu chafika pa 20 tsopano. Azibambo enanso awiri ali pa ukaidi wosachoka panyumba. A Mboni enanso okwana 15, ena mwa iwo a zaka za m’ma 70 ndi 80, analamulidwa kuti asainire chikalata chosonyeza kuti sachoka m’dera lomwe amakhala. Pofika pa 14 June, 2018, akuluakulu a boma la Russia akhala akunena kuti a Mboni oposa 40 anapalamula milandu ndipo ngati angapezeke olakwa, akakhala m’ndende mpaka zaka 10.

Boma la Russia lachita zosemphana ndi zimene linanena kuti ngakhale kuti litseka malo onse ovomerezeka a Mboni za Yehova, zimenezi sizikutanthauza kuti liletsa wa Mboni wina aliyense kuchita zinthu zogwirizana ndi chikhulupiriro chake. Apatu bomali lachita zosiyana kwambiri ndi zimene linanena ndipo lagwiritsa ntchito molakwika Gawo 282 la Malamulo a Zaupandu pofuna kuimba a Mboni mlandu wochita nawo, kutsogolera, kapena kupereka ndalama zothandizira gulu lomwe “limachita zinthu zoopsa.” Zoona zake n’zakuti m’malo molimbana ndi anthu ochita zinthu zoopsa, boma la Russia likuzunza nzika zake zomwe, chifukwa cholambira Mulungu mwamtendere.

Madera Amene Apolisi Anathyola Nyumba, Kumanga Anthu Komanso Kukawasunga M’ndende Posachedwapa

Ku Saratov, pa 12 June, 2018. Apolisi analowa komanso kufufuza m’nyumba za a Mboni ndipo anagwira a Mboni osachepera 10, n’kupita nawo ku polisi kuti akawafunse mafunso. Pamene ankafufuza m’nyumba ina, akuluakulu a boma anaika m’nyumbamo mabuku a Mboni oletsedwa ndi makhoti a ku Russia komanso anagwira azibambo 5 a Mboni n’kukawatsekera. Kenako apolisi anamasula azibambo awiri koma anasunga a Konstantin Bazhenov ndi a Felix Makhammadiev powaganizira kuti anapalamula mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa.’ Anasunganso a Aleksey Budenchuk popanda kuwauza mlandu womwe anapalamula. Pa 14 June, 2018, khoti la m’boma la Frunzenskiy mumzinda wa Saratov linalamula kuti a Bazhenov ndi a Makhammadiev awasunge kaye m’ndende mpaka pa 12 August, 2018 poyembekezera kuwazenga mlandu. Khotili linalamulanso kuti a Budenchuk asungidwebe m’ndende koma tsiku lodzawatulutsa silikudziwika. Apolisi analamula wa Mboni winanso kuti asainire chikalata chosonyeza kuti satuluka m’deralo.

Ku Tomsk, pa 3 June, 2018. Nthawi ya 10:00 m’mawa, apolisi ndi gulu linalake la asilikali oopsa kwambiri (Spetsnaz) analowa m’nyumba ziwiri za a Mboni za Yehova m’dera la Tomsk, ku Siberia. Iwo anagwira a Mboni pafupifupi 30 kuphatikizapo mayi wazaka 83. Apolisiwo analanda katundu m’nyumba komanso m’magalimoto a a Mboni za Yehova, kuwakweza m’mabasi, n’kupita nawo ku malo othana ndi anthu ochita zinthu zoopsa. (Center for Counteracting Extremism)

Atafika kumalowa, a Ivan Vedrentsev, a Aleksandr Ivanov, ndi a Vyacheslav Lebedev omwe ankafufuza za nkhaniyi, anapanikiza a Mboni ena ndi mafunso mpaka 2:00 m’bandakucha. Ofufuzawo anaopseza wa Mboni wina kuti achotsedwa ntchito. Pa nthawiyi ma ambulansi ankatumizidwa kumalowo maulendo angapo ndipo wa Mboni m’modzi anagonekedwa m’chipatala.

M’modzi mwa a Mboni omwe anamangidwa, a Sergey Klimovu, anawatsekera m’chitokosi. Pa 5 June, 2018, khoti la m’boma la Oktyabrskiy mumzinda wa Tomsk linalamula kuti a Klimovu aikidwe m’ndende mpaka pa 4 August, 2018 poyembekezera kuwazenga mlandu. Iwo akuwaganizira kuti anapalamula mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa.’ Woweruza milandu anakana maganizo oti a Klimovu apatsidwe chilango cha ukaidi wosachoka panyumba kapenanso kuti awatulutse pabelo.

Pa 3 June, 2018, ku Pskov. Apolisi analowa m’nyumba zambiri za a Mboni za Yehova ku Pskov. Atafika panyumba ina, aliyense amene anam’peza panyumbapo anamangidwa komanso kufunsidwa mafunso, kuphatikizapo anthu ena awiri omwe si a Mboni. A Mboni za Yehova ambiri, kuphatikizapo a Gennadiy Shpakovsky, anawatengera ku likulu la zachitetezo m’deralo (Pskov Regional Headquarters of the Federal Security Services, FSB) kuti akawafunse mafunso. Ena mwa anthu omwe anawatengera kupolisiko anawakakamiza kuti apereke umboni wosonyeza kuti a Shpakovsky anali wolakwa. Akuluakulu a boma anatsegulira a Shpakovsky mlandu powaganizira kuti ‘amatsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa.’ Ngakhale kuti pambuyo pake anatulutsidwa, akuluakulu a bomawa akhoza kuwaganiziranso milandu ina nthawi iliyonse.

Ku Khabarovsk, pa 30 May, 2018. Apolisi anamanga a Ivan Puyda pambuyo polowa m’nyumba mwawo n’kuchitamo chipikisheni. Kenako anawatengera ku Magadan, komwe anakawatsekera m’chitokosi. Pa 1 June, 2018, khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy linalamula kuti a Puyda asungidwe m’ndende mpaka pa 30 July, 2018 powaganizira kuti ‘amatsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa.’

Ku Magadan, pa 30 May, 2018. Apolisi onyamula mfuti komanso ovala zobisa nkhope analowa m’nyumba za anthu m’dera la Magadan ndipo anamanga ndi kutsekera a Konstantin Petrov, a Yevgeniy Zyablov, ndi a Sergey Yerkin. Ndipo pa 1 June, 2018, khoti la mumzinda wa Magadan linatsekera bambo Petrov ndi bambo Zyablov powaganizira kuti ‘amatsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa.’ Pa tsiku lomwelinso, khoti la m’boma la Magadanskiy linanenanso kuti a Yerkin akuwaganizira kuti nawonso anapalamula mlandu womwewu. Ndipo a Mboni onse atatuwa anauzidwa kuti asungidwa m’ndende mpaka pa 29 July, 2018 poyembekezera kuti awazenge mlandu.

A Dmitriy Mikhailov

Dera la Shuya, M’chigawo cha Ivanovo, pa 29 May, 2018. Akuluakulu a boma anatenga a Dmitriy Mikhailov n’kukawatsekera m’chitokosi kachiwiri. Pa 20 April apolisi atalowa mwankhanza m’nyumba yawo, anawauza kuti apalamula mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa’ ndipo anawauza kuti asaine chikalata chosonyeza kuti sadzatuluka m’dera lawo. Pomwe pa 29 May, akuluakulu a boma anawauza kuti apalamulanso mlandu ‘wopereka ndalama kugulu lochita zinthu zoopsa.’ Ndipo pa 3 June, 2018, khoti la mumzinda wa Shuya linalamula kuti a Mikhailov asungidwe m’ndende mpaka pa 19 July, 2018 poyembekezera kuwazenga mlandu.

Ku Naberezhnye Chelny, Republic of Tatarstan, pa 27 May, 2018. Usiku wa patsikuli, nthumwi za bungwe loona zachitetezo (FSB) linachita chipikisheni m’nyumba za anthu ndipo zinalanda zinthu monga mafoni, zipangizo zina zamakono ndiponso ziphaso zoyendera. Patsikuli, a Ilkham Karimov, a Konstantin Matrashov, ndi a Vladimir Myakushin anamangidwa n’kukatsekeredwa m’chitokosi. Pa 29 May, 2018, khoti la m’boma la Naberezhnochelninskiy linanena kuti azibambo atatuwa apalamula mlandu wotsogolera ndi kulimbikitsa anthu kuti alowe m’gulu “lochita zinthu zoopsa” komanso kuti nawonso anachita nawo zoopsazo. Khotili linalamula kuti anthuwa asungidwe m’ndende mpaka pa 25 July, 2018 poyembekezera kuzengedwa mlandu. Kenako a Aydar Yulmetyev nawonso anamangidwa ndipo pa 31 May, 2018 khoti linalamula kuti nawonso asungidwe m’ndende.

Ku Perm, pa 22 May, 2018. Pamene ankachokera ku Moldova pobwerera ku Perm, a Aleksandr Solovyev ndi akazi awo a Anna anakumana ndi apolisi pasiteshoni ya sitima. Kenako apolisiwo anamanga ndi unyolo bambo Solovyev, kuwalanda zinthu zawo komanso anasiyanitsa banjali powakweza m’magalimoto osiyana n’kupita nawo ku polisi. Pamene apolisi ankachita chipikisheni kunyumba kwawo, bambo Solovyev anawatsekera m’ndende ndipo akazi awo ankawafunsa mafunso. Pa 24 May, 2018, khoti la mumzinda wa Sverdlovskiy linanena kuti bambo Solovyev anapalamula mlandu ‘wochita zinthu ndi gulu lomwe limachita zinthu zoopsa’ ndipo linawapatsa chilango cha ukaidi wosachoka panyumba.

Ku Birobidzhan, pa 17 May, 2018. Apolisi 150 komanso mamembala a gulu la FSB, analowa m’nyumba 22 za a Mboni za Yehova ndipo ankayenda limodzi ndi anthu ena ake omwe anagwirizana nawo kuti aziyerekezera ngati a Mboni omwe awagwira kale. Apolisiwo analanda matabuleti, mafoni a m’manja ndiponso ndalama. M’modzi mwa a Mboni 34 omwe nyumba zawo zinafufuzidwa, a Alam Aliev anawagwira n’kuwaika m’ndende. Pa 18 May, khoti la ku Birobidzhanskiy linanena kuti a Aliev anapalamula mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lochita zinthu zoopsa’ ndipo linalamula kuti asungidwe m’ndende mpaka pa 13 July, 2018 poyembekezera kuwazenga mlandu. Pa 25 May, 2018, woweruza milandu wina dzina lake A. V. Sizova wa Khoti la Apilo lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda anavomera apilo yomwe bambo Aliev anapanga ndipo anagamula kuti asakhalenso m’ndende.

Ku Orenburg pa 16 May, 2018. Apolisi analowa komanso kuchita chipikisheni m’nyumba za a Mboni ndiponso anamanga a Mboni atatu omwe mayina awo ndi: Aleksandr Suvorov, Vladimir Kochnev, komanso Vladislav Kolbanov. Pa 18 May, khoti la ku Promyshlenniy linanena kuti a Kolbanov anapalamula mlandu ‘wopereka ndalama zothandizira zinthu zoopsa.’ Khotili linawatulutsa m’ndende koma linalamula kuti akhale pa ukaidi wosachoka panyumba. Tsiku lotsatira, khoti lomweli linanena kuti a Kochnev ndi a Suvorov anapalamula mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lochita zinthu zoopsa’ ndipo linalamula kuti aikidwe m’ndende mpaka pa 14 July, 2018 poyembekezera kuwazenga mlandu. Wofufuza mlanduwu analamulanso a Mboni ena 7 kuti asainire chikalata chovomereza zoti satuluka mumzindamo pa nthawi yofufuza mlanduwu.

Kumanzere: A Aleksandr Suvorov; Kumanja: A Vladimir Kochnev

Kodi Zimene Mayiko Ena Alankhulapo Zithandiza?

Bungwe la European Union (EU) ndi dziko la United States alemba makalata odzudzula boma la Russia chifukwa chosalemekeza ufulu wa anthu. Bungwe la EU linapempha dziko la Russia “kuti lilemekeze zimene linalonjeza kuti lizitsatira zimene mayiko anagwirizana pa nkhani ya ufulu wopembedza kapena wochita zimene munthu amakhulupirira, ufulu wolankhula komanso ufulu wosonkhana.” Nalonso dziko la United States linauza dziko la Russia “kuti litulutse mofulumira anthu onse omwe anamangidwa chifukwa choti anangochita zinthu zogwirizana ndi ufulu wawo wopembedza kapena wochita zimene amakhulupirira.”

Loya woimira Mboni za Yehova a Philip Brumley anati: “A Mboni za Yehova padziko lonse ndi okhudzidwa kwambiri ndi kuzunzidwa kwa a Mboni anzawo ku Russia. Panopa, a Mboni za Yehova akuchitidwa nkhanza zomwenso anavutika nazo pa nthawi ya ulamuliro wa boma la Chikomyunizimu. Zimene boma la Russia likuchita popitiriza kuchita nkhanza, zikusonyezeratu kuti likunyalanyaza malamulo ake okhudza kulemekeza ufulu wachibadwidwe.”

A Mboni omwe anaikidwa m’ndende m’mbuyomu poyembekezera kuzengedwa mlandu *

 • A Dennis Christensen

  Ku Oryol. Ali ndi zaka 45, anawatsekera pa 25 May, 2017 ndipo analamulidwa kuti akhalebe m’ndende mpaka pa 1 August, 2018.

 • A Valentin Osadchuk

  Ku Vladivostok. Ali ndi zaka 42, anawatsekera pa 19 April, 2018 ndipo analamulidwa kuti akhalebe m’ndende mpaka pa 20 June, 2018.

 • A Viktor Trofimov

  Ku Polyarny. Ali ndi zaka 61, anawatsekera pa 18 April, 2018 ndipo analamulidwa kuti akhalebe m’ndende mpaka pa 11 October, 2018.

 • A Roman Markin

  Ku Polyarny. Ali ndi zaka 44, anawatsekera pa 18 April, 2018 ndipo analamulidwa kuti akhalebe m’ndende mpaka pa 11 October, 2018.

 • A Anatoliy Vilitkevich

  Ku Ufa. Ali ndi zaka 31, anawatsekera pa 10 April, 2018 ndipo analamulidwa kuti akhalebe m’ndende mpaka pa 2 July, 2018.

^ ndime 21 Kuti mudziwe zambiri pitani pa Malo a Nkhani pa jw.org ndipo werengani nkhani yamutu wakuti: “Apolisi Ayamba Kuchitira Nkhanza a Mboni za Yehova ku Russia.”