Pitani ku nkhani yake

Nyumba ya Misonkhano ya Kolomyazhskiy ku St. Petersburg

DECEMBER 25, 2017
RUSSIA

Akuluakulu a boma la Russia Alanda Nyumba ya Misonkhano ya Mboni za Yehova

Akuluakulu a boma la Russia Alanda Nyumba ya Misonkhano ya Mboni za Yehova

Pa 14 December 2017, akuluakulu a boma la Russia anathyola mpanda n’kulowa m’Nyumba ya Misonkhano ya Kolomyazhskiy ku St. Petersburg. Akuluakuluwo anazungulira malowo n’cholinga choti anthuwo asathawe. Koma palibe wa Mboni aliyense amene anavulala pa nthawi ya chipoloweyi ndiponso nyumba yochitiramo misonkhanoyo siinawonongedwe.

Chithunzi cha apolisi a ku Russia chojambulidwa ndi kamera yachitetezo

Chinthu chachikulu chomwe akuluakulu a boma la Russia alanda, ndi Nyumba ya Misonkhanoyi. Izi zachitika kuchokera pomwe komiti ya Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia inapereka chigamulo chake pa 17 July 2017. Khotili linagamula kuti mabungwe onse a Mboni za Yehova atsekedwe m’dziko la Russia, ntchito zawo ziletsedwe komanso maofesi awo alandidwe.

Apolisi ali mkati mwa Nyumba ya Misonkhano

Nyumba ya Misonkhanoyi inakonzedwanso mu 2002 ndipo mumakwana anthu 1,500. Nyumbayi yakhala ikugwiritsidwa ntchito pochita misonkhano ikuluikulu komanso mipingo ya m’deralo imachitiramo misonkhano yawo. Maloya oimira a Mboni anazindikira kuti akuluakulu a bomawo anakasintha dzina la Nyumba ya Misonkhanoyo m’kaundula wa boma n’kuikapo dzina losonyeza kuti nyumbayo ili m’manja mwa dziko la Russia. Kuchokera nthawi imeneyo nyumbayo inagulitsidwa ku chipatala china cha pafupi ndi malowo. Panopa akuluakulu a chipatalachi anaika chikwangwani chawo pa geti la Nyumba ya Misonkhanoyo.

Patadutsa wiki imodzi kuchokera pamene khoti linapereka chigamulo choopseza kuti litenga maofesi a Mboni n’kuwasandutsa kukhala maofesi a boma, akuluakulu a boma analanda Nyumba ya Misonkhano. Nyumbayi ili pafupi ndi St. Petersburg. Chigamulo chimene khotili linapereka chinasokoneza pangano la zaka 17 lomwe likulu la Mboni za Yehova m’dziko la Russia linasainirana ndi bungwe la Watchtower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ngati mlanduwu sungakomere a Mboni, ndiye kuti zipereka mwayi kwa akuluakulu a boma la Russia kuti alandenso maofesi komanso zinthu zina za a Mboni.

A Mboni za Yehova akuona kuti zimene boma la Russia likuchitazi zikuonetseratu kuti amadana ndi chipembedzo chawo ndipo zimenezi zachititsa kuti asakhale ndi ufulu wachipembedzo komanso kuti nyumba yomwe amagwiritsa ntchito ilandidwe. Komatu ndalama zomwe zinagwiritsidwa ntchito pogula komanso kukonzanso nyumbayi zinaperekedwa ndi nzika za ku Russia komweko zomwenso ndi zosauka. A Mboni za Yehova akuyesetsa kugwiritsa ntchito njira iliyonse yomwe ingapezeke kuchita apilo pa nkhanza zomwe bomali likuchita. Iwo akutumiza madandaulo awo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe komanso ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu.