Woimira Boma pa Milandu ku Russia analemba kalata yoopseza kuti atseka likulu la a Mboni za Yehova a m’dzikolo. A Mboniwo anakachita apilo ku khoti lina la m’boma la Tver mu mzinda wa Moscow za nkhaniyi. Pa nthawi yomvetsera mlanduwu, akuluakulu ogwira ntchito ku maofesi a akazembe a mayiko ena analikonso ku khotiko. Kenako Khotilo linanena kuti lidzapitiriza kuzenga mlanduwo pa 23 September, 2016, ndipo lidzamvetsera mlanduwu kuchokera ku mbali zonse ziwiri.

Posachedwapa boma lakhala likuchita zinthu zina zimene zikusokoneza ufulu wolambira wa a Mboni. Malamulo okonzedwanso a dzikolo okhudza ufulu umene munthu ali nawo wotsatira zimene amakhulupirira komanso okhudza zipembedzo, anayamba kugwira ntchito pa 20 July, 2016. Tikuyembekezera mwachidwi kuona akuluakulu a boma la Russia akutsatira malamulo okonzedwansowa pamene akuchita zinthu ndi a Mboniwo.