Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

NOVEMBER 18, 2013
PADZIKO LONSE

Musaiwale Anthu Amene Ali Kundende

Musaiwale Anthu Amene Ali Kundende

Gawo 18 la Pangano la Padziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale limanena kuti munthu aliyense ali ndi “ufulu wonena maganizo ake, wotsatira chikumbumtima chake, komanso wolowa chipembedzo chimene akufuna.” * M’mayiko ena a Mboni za Yehova akamagwiritsira ntchito ufulu umenewu amamangidwa ngakhalenso kuchitiridwa zinthu za nkhanza. Ambiri mwa anthu amene amamangidwawa ndi anyamata amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ena amamangidwa chabe chifukwa choti akutsatira zimene amaphunzira m’Baibulo.

Zinthu za nkhanza zimene a Mboni za Yehova amachitiridwa sizimawalepheretsa kutsatira zimene amakhulupirira. M’malomwake, zimawononga mbiri ya mayiko amene amalephera kulemekeza ufulu wachibadwidwe wa anthu. Tchati chili m’munsichi chikusonyeza mayiko amene a Mboni za Yehova anamangidwa komanso chiwerengero cha amene anamangidwawo.

DZIKO

AMENE ANAMANGIDWA

 Eritrea

52

 Korea, South

599

 Nagorno-Karabakh

1

 Singapore

18

 Turkmenistan

9

Onse Pamodzi

679

Anthu amene anamangidwa pofika pa November 12, 2013

 ERITREA

Malinga ndi lipoti laposachedwapa, anthu 52 a Mboni za Yehova, amuna ndi akazi omwe, anamangidwa ndipo akukhala mozunzika kwambiri. Ngakhale kuti palibe amene anapititsidwa kukhoti kukazengedwa mlandu, anthuwa anamangidwa chifukwa chokana kuchita zinthu zina potsatira zimene amakhulupirira, chifukwa chochita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo kapena pa zifukwa zimene sananene. Azibambo atatu, omwe ndi a Paulos Eyassu, a Isaac Mogos, ndi a Negede Teklemariam, akhala ali m’ndende kwa zaka pafupifupi 20 chifukwa anakana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Iwo anamangidwa pa September 24, 1994. Anthu ena awiri a Mboni za Yehova omwe mayina awo ndi a Misghina Gebretinsae ndi a Yohannes Haile omwe ndi a zaka zoposa 60 anafera kundende. Dziko la Eritrea lakhala likumanga, kuzunza komanso kuchitira chipongwe anthu a Mboni za Yehova kuyambira nthawi imene dzikoli linalandira ufulu wodzilamulira mu 1993.

 SOUTH KOREA

Pakali pano, anyamata 599 a Mboni ali m’ndende ndipo aliyense anauzidwa kuti akhale m’ndende kwa miyezi 18 chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Kungoyambira nthawi imene ku Korean kunali nkhondo mpaka pano, dziko la South Korea lakhala likuimba mlandu anyamata a Mboni za Yehova amene amakana kulowa usilikali ndipo dzikoli silinakhazikitse ntchito zoti anthu okana usilikali azigwira. Pa nthawi yonseyi, dziko la South Korea lamanga a Mboni 17,549 ndipo kuphatikiza pamodzi onse akhala m’ndende zaka 34,100 chifukwa anakana kulowa usilikali. Dziko la South Korea lalephera kutsatira mgwirizano wake wa padziko lonse ndipo silikufuna kulemekeza ufulu wa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti Mayiko ndi Mabungwe Akudzudzula Dziko la South Korea Chifukwa cha Zinthu Zopanda Chilungamo Zimene Likuchita.

 NAGORNO-KARABAKH

Mnyamata wa zaka 20 wa Mboni ali ku ndende chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Dziko la Nagorno-Karabakh silinakhazikitse ntchito zoti anthu amene amakana kulowa usilikali azigwira. Pa December 30, 2011, mnyamatayu anaweruzidwa kuti akakhale kundende miyezi 30 ndipo pa January 29, 2013 anakanizidwa atapempha kuti atuluke. Mnyamatayu anapempha kutuluka chifukwa amadwala koma akuluakulu oyang’anira ndendeyo anamukaniza.

 SINGAPORE

Boma la Singapore limakakamiza anthu kulowa usilikali ndipo silipereka ufulu kwa anthu amene safuna kulowa usilikali chifukwa chofuna kutsatira zimene amakhulupirira. Anyamata 18 amene amalambira Mulungu ndi a Mboni za Yehova ali kundende zoyang’aniridwa ndi asilikali ndipo analamulidwa kuti aliyense akhaleko miyezi 39. Iwo anawamanga chifukwa anakana kuchita zinthu zosiyana ndi zimene anaphunzira m’Baibulo. Mnyamata wina wa Mboni anatulutsidwa kundende mu August 2013 pambuyo pomangidwa chaka chimodzi chifukwa kugwira kachiwiri usilikali.

 TURKMENISTAN

Pakali pano amuna 9 a Mboni m’dziko la Turkmenistan ali kundende, 8 amangidwa chifukwa chokana kuchita zosiyana ndi zimene amakhulupirira ndipo m’modzi chifukwa cha mlandu wongomunamizira. Anthuwa analamulidwa kuti akhale kundende miyezi pakati pa 12 ndi 24 ndipo nthawi zambiri amamenyedwa mopanda chifundo ndi alonda a kundendeko komanso asilikali. Akatulutsidwa, anthu omwewa akhala akuimbidwa mlandu ngati akabwerebwere ndipo amaikidwa m’ndende zovuta kwambiri.

^ ndime 2 Onaninso Gawo 18 la Chikalata cha Mfundo za Ufulu Wachibadwidwe cha United Nations, ndi Gawo 9 la Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.