Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

NAGORNO-KARABAKH

Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Achinyamata a Mboni za Yehova ku Nagorno-Karabakh omwe afika msinkhu woti akhoza kulowa usilikali akumangidwa akakana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Malamulo a m’dzikoli sapereka ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira ndipo munthu akakana kulowa usilikali samupatsa mwayi wogwira ntchito zina m’malo mwa usilikaliwo. Chifukwa cha zimenezi, achinyamata a Mboni amawatsekera m’ndende chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira zoti sayenera kuphana.

Anawakaniza Kugwira Ntchito Zina

Pa January 29, 2014, dipatimenti ina ya asilikali ya mumzinda wa Askeran inalamula a Artur Avanesyan, omwe ndi a Mboni za Yehova, kuti akayambe usilikali. Tsiku lotsatira, a Avanesyan analemba kalata yopempha kuti awapatse ntchito ina m’malo mogwira ntchito ya usilikali. Loya wawo anakumana ndi akuluakulu a asilikali ku Nagorno-Karabakh ndi ku Armenia ndipo zinkaoneka ngati a Avanesyan awapatsa ntchito ina m’malo mwa usilikali ku Armenia.

Chifukwa chakuti a Avanesyan ankayembekezera kuti zinthu ziyenda bwino, anasamukira ku Armenia ndipo pa February 13, 2014 ali konko, analemba kalata ku dipatimenti yoona zopatsa ntchito zina anthu okana kulowa usilikali. M’malo moitanidwa kuti akawapatse ntchito zina, a Avanesyan anaitanidwa kuti akaonekera ku polisi yaikulu ya ku Yerevan pa July 14, 2014. Atafika ku polisiko anapeza apolisi a ku Nagorno-Karabakh akuwayembekezera ndipo anawamanga n’kubwerera nawo ku Nagorno-Karabakh. Tsiku lotsatira anawatsekera m’ndende imene amaikamo anthu amene atsala pang’ono kuwazenga milandu ndipo anakonza zoti akawaimbe mlandu ku khoti laling’ono la ku Nagorno-Karabakh.

Pa nthawi imene ankaimbidwa mlanduwo, a Avanesyan anatulukira kuti miyezi 4 m’mbuyomo, khotili linali litalamula kuti amangidwe ndiponso kukhala m’ndende kuti aziyembekezera kuimbidwa mlandu. Khotilo linawauzadi a Avanesyan zimene linanena miyezi 4 zija zakuti amangidwe ndipo nthawi yomweyo anamangidwa. Khotili linakana apilo imene a Avanesyan anachita yopempha kuti asakakhale kundende poyembekezera kuimbidwa mlandu.

Pa September 30, 2014, khotili linagamula kuti a Avanesyan akakhale kundende kwa miyezi 30. Panopa a Avanesyan anachita apilo mlanduwo. Iwowo, anthu a m’banja lawo komanso a Mboni za Yehova padziko lonse, akuyembekezera kuti khotili lidzasintha chigamulo chake n’kuwalola kuti azigwira ntchito zina m’malo mwa usilikali kusiyana n’kuti azivutika kundende chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira zomwe ndi zochokera m’Baibulo.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. December 25, 2014

  Khoti lalikulu ku Nagorno-Karabakh linagwirizana ndi zimene khoti lina linagamula kuti a Artur Avanesyan akhale m’ndende kwa miyezi 30.

 2. September 30, 2014

  Khoti laling’ono la dziko la Nagorno-Karabakh ku Martakert linagamula kuti a Artur Avanesyan akhale m’ndende kwa miyezi 30.

 3. July 14, 2014

  A Artur Avanesyan anamangidwa ku Armenia ndipo anatumizidwa ku Nagorno-Karabakh kuti akakhale m’ndende poyembekezera kuimbidwa mlandu.

 4. December 30, 2011

  Karen Harutyunyan, amene ndi wa Mboni ndipo ali ndi zaka 18, anakana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira. Chifukwa cha zimenezi analamulidwa kuti akhale m’ndende kwa miyezi 30.

 5. February 16, 2005

  Areg Avanesyan amene ndi wa Mboni za Yehova anakana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira ndipo anamulamula kuti akhale m’ndende miyezi 48.

 6. June 12-13, 2001

  Amboni atatu analamulidwa kuti akhale m’ndende kwa miyezi 6 ndipo ena mpaka chaka. Anawalamula zimenezi chifukwa anakana kuchita maphunziro ausilikali potsatira zimene amakhulupirira.