Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

SEPTEMBER 12, 2016
NAGORNO-KARABAKH

Artur Avanesyan Amukhululukira ndipo Watulutsidwa M’ndende

Artur Avanesyan Amukhululukira ndipo Watulutsidwa M’ndende

Akuluakulu a boma la Nagorno-Karabakh anakhululukira Artur Avanesyan yemwe anali m’ndende ya Shushi ndipo anamutulutsa pa 6 September, 2016. Artur, yemwe ali ndi zaka 20, anamulamula kuti akakhale m’ndende kwa miyezi 30 chifukwa chokana ntchito ya usilikali. Pamene ankamukhululukira n’kuti atagwira ukaidi kwa miyezi 26. Asanamangidwe, iye anapempha akuluakulu a boma kuti amupatse ntchito zina m’malo mwa usilikali koma zimenezi sizinatheke. Panopo wachinyamatayu akusangalala kwambiri chifukwa chokhalanso limodzi ndi banja lake.

A Mboni za Yehova akuthokoza kuti Artur watulutsidwa m’ndende. Iwo akukhulupirira kuti akuluakulu a dziko la Nagorno-Karabakh azilemekeza ufulu umene achinyamata ali nawo wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo aziwapatsa ntchito zina osati kuwakakamiza kulowa usilikaliwo.