Pitani ku nkhani yake

KYRGYZSTAN

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni za Yehova ku Kyrgyzstan

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni za Yehova ku Kyrgyzstan

A Mboni za Yehova akhala akupezeka ku Kyrgyzstan kuyambira mu 1956 ndipo analembetsa monga chipembedzo chovomerezeka mu 1998. Ngakhale kuti m’mbuyomu ufulu wawo wopembedza wakhala ukuphwanyidwa, posachedwapa boma lakhala likuyesetsa kuteteza maufulu awo.

Mu November 2013, Komiti ya Khoti Lalikulu Kwambiri Yoona za Malamulo ku Kyrgyzstan inagamula kuti lamulo lokhudza kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali ndi losagwirizana ndi malamulo oyendetsera dzikolo ndipo linauza boma kuti lisinthe lamuloli. Makhoti a ku Kyrgyzstan anayamba kutsatira chigamulochi ndipo kuyambira chakumayambiriro kwa chaka cha 2014, a Mboni sakumaimbidwanso milandu chifukwa chokana kugwira ntchito ya usilikali. Pa 29 June, 2015, dziko la Kyrgyzstan linasintha lamulo lokhudza kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali kuti anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azipatsidwa ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali.

Mu September 2014, Komiti ya Khoti Lalikulu Kwambiri Yoona za Malamulo inagamula mokomera a Mboni za Yehova komanso ufulu wachipembedzo ponena kuti zigawo zina za lamulo lokhudza chipembedzo lomwe linakhazikitsidwa mu 2008 ndi losagwirizana ndi malamulo oyendetsera dzikolo. Komabe, komiti ina yoona za zipembedzo m’dzikolo (State Committee on Religious Affairs) siinalabadire chigamulo chimenechi ndipo yakana kulemba mabungwe a Mboni omwe ali kum’mwera kwa dzikoli kuti akhale ovomerezeka ndi boma. Zimenezi zimachititsa kuti akuluakulu ena aziona kuti ntchito ya a Mboni ndi yosavomerezeka mwalamulo. Komabe, a Mboni akakambirana ndi akuluakuluwa zokhudza nkhaniyi, nthawi zambiri amawalola kusonkhana pamodzi kuti alambire Mulungu komanso kuuza ena zomwe amakhulupirira popanda chowasokoneza. A Mboni akukukhulupirira kuti boma lidzayamba kutsatira chigamulo cha Komiti Yoona za Malamulo ndipo lidzalemba mabungwe a Mboni omwe ali kum’mwera kwa dziko la Kyrgyzstan kuti akhale ovomerezeka ndi boma.