Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MARCH 1, 2016
KYRGYZSTAN

Kodi Apolisi Amene Anachitira Nkhanza a Mboni a ku Osh Adzapatsidwa Chilango?

Kodi Apolisi Amene Anachitira Nkhanza a Mboni a ku Osh Adzapatsidwa Chilango?

Loya wamkulu wa boma la Kyrgyzstan walamulanso kachitatu loya wa boma wamumzinda wa Osh kuti afufuze zimene apolisi 10 anachita kuti aone ngati ayenera kuwatsegulira mlandu. Mu August 2015, apolisiwo anasokoneza msonkhano wachipembedzo wa a Mboni za Yehova ndipo anamenya anthu ambiri amene anasonkhana pamalopo. Ngakhale kuti pali umboni wokwanira wakuti apolisiwo anachitadi zinthu zankhanza, loya wa boma wamumzinda wa Osh akukana kufufuza nkhaniyi.

Apolisi Anasokoneza Msonkhano wa a Mboni N’kuwachitira Nkhanza

Lamlungu m’mawa pa 9 August 2015, apolisi okwana 10 a ku Osh a m’Dipatimenti 10, anasokoneza msonkhano wachipembedzo umene a Mboni oposa 40 ankachita mwamtendere palesitilanti ina imene anachita lendi. Mmodzi wa apolisiwo anauza Nurlan Usupbaev, yemwe ankachititsa msonkhanowo, kuti auimitse mwamsanga chifukwa choti ndi wosemphana ndi malamulo a boma. Ndiyeno apolisiwo anayamba kuopseza kuti awombera aliyense yemwe anali pamsonkhanowo. Munthu wina dzina lake Tynchtyk Olzhobayev yemwe anali pamsonkhanowu ankafuna kujambula nkhanza zimene apolisiwo ankachita ndipo iwo anamutengera kuchipinda china n’kuyamba kumumenya koopsa.

Apolisiwo anagwira amuna 10 a Mboni n’kupita nawo kupolisi. Kumeneko anayamba kumenya mwankhanza a Mboni 6 ndipo atatu, kuphatikizapo a Usupbaev, anawakanyanga pakhosi. Amunawo anawatulutsa kupolisiko tsiku lomwelo ndipo amene anavulala kwambiri anapita kuchipatala kuti akalandire chithandizo.

Patadutsa masiku awiri, pa 11 August, Kozhobek Kozubayev komanso Nurbek Sherikbayev omwe ndi apolisi amene anatsogolera posokoneza komanso kumenya a Mboniwo, anagwira a Usupbaev ponena kuti ali ndi mlandu wochita zachipembedzo zosemphana ndi malamulo. A Usupbaev anauzidwa kuti mlandu wawo udzazengedwa pa 20 ndi pa 21 August kukhoti lamumzinda wa Osh.

Makhoti Anagamula Kuti A Mboni Ali ndi Ufulu Wolambira

Pa nthawi yozenga mlanduwu, woimira Dipatimenti 10 ananena kuti msonkhano wachipembedzo umene unachitika pa 9 August unali wosemphana ndi malamulo chifukwa choti chipembedzo cha Mboni za Yehova sichinalembedwe m’kaundula wa ku Osh. Ananenanso kuti a Mboniwo anaphwanya malamulo a boma la Kyrgyzstan onena kuti anthu sayenera kukopa ana kuti alowe m’chipembedzo chinachake. Ananena zimenezi chifukwa choti a Mboniwo anali limodzi ndi ana awo pamsonkhanowo.

Pa 21 August, woweruza wa khoti lamumzinda wa Osh anapeza kuti a Usupbaev alibe mlandu. Khotili linagamula kuti mlanduwu uthe chifukwa chakuti panalibe umboni woti a Usupbaev ankachita zachipembedzo zosemphana ndi malamulo kapenanso kukopa ana kulowa m’chipembedzo chawo.

Loya wa boma wamumzinda wa Osh sanagwirizane nazo zoti a Usupbaev alibe mlandu ndipo anachita apilo nkhaniyi kukhoti lalikulu lam’deralo. Koma khotili linakana apiloyo ndipo linagwirizana ndi chigamulo cha khoti linalo choti a Usupbaev alibe mlandu. Khoti lalikululi linanena kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi chovomerezeka ndipo chinalembedwa m’kaundula wam’dziko la Kyrgyzstan. Khotili linanenanso kuti khoti lalikulu lam’dzikoli linali litagamula kale kuti lamulo la Kyrgyzstan lonena kuti zipembedzo ziyenera kulembedwanso m’kaundula wa m’dera limene zili ndi losemphana ndi malamulo ena a boma. * Ngakhale zili choncho, loyayo wachitanso apilo nkhaniyi kukhoti lalikulu lam’dzikoli ndipo lidzamva mlanduwu pa 2 March 2016.

Loya wa Boma ku Osh Analamulidwa Kuti Afufuze Zimene Apolisi Anachita

Pa nthawi imene mlandu wa a Usupbaev unali mkati, iwo limodzi ndi anthu ena amene anamenyedwa kwambiri pa 9 August analemba chikalata chodandaula ku ofesi ya loya wa boma mumzinda wa Osh. Anthuwo anapempha kuti apolisi 10 amene anawachitira nkhanza aja aimbidwe mlandu. Koma loya wa boma wamumzinda wa Osh wakhala akukana katatu konse kutsegula mlanduwu ndipo ulendo uliwonse a Mboniwo ankachita apilo kwa loya wamkulu wa boma. Kawiri konse loya wamkuluyo ankasintha chigamulo cha loya wamumzinda wa Osh n’kumuuza kuti aiganizirenso bwino nkhaniyo. Koma a Mboni atachitanso apilo kachitatu, loya wamkuluyo sanagamule yekha nkhaniyo, m’malomwake anangoibweza kwa loya wamumzinda wa Osh uja kuti aiganizirenso. Zimene loya wamkuluyo anachita pa 21 January 2016 posiya nkhaniyi m’manja mwa loya wamumzinda wa Osh, zikuchititsa a Mboniwo kukayikira zoti apolisiwo adzalangidwa chifukwa cha nkhanza zimene anachita.

A Mboni za Yehova ku Kyrgyzstan akusangalala chifukwa choti chipembedzo chawo chinalembedwa m’kaundula wa m’dzikoli komanso kuti makhoti a ku Osh anagamula mlandu wawo mowakomera. Iwo akuyamikira kuti oweruza achilungamo akuthandiza kuti m’dzikoli mukhale ufulu wachipembedzo. Akuyamikira chifukwa choti oweruzawo akugamula motsatira malamulo komanso lonjezo la bomali loti azipatsa anthu ufulu wolambira ndiponso wokhulupirira zimene akufuna. Komabe a Mboni akudandaula kuti akuluakulu a boma sakuchitapo kanthu pa nkhani ya apolisi amene anachitira nkhanza a Mboni. Choncho a Mboni za Yehova akupempha loya wamkulu wa boma kuti achitepo kanthu popereka chilango kwa apolisiwo.

^ ndime 10 Dipatimenti 10 ndi nthambi ya Unduna Woona za M’dziko ku Kyrgyzstan.

Khoti lalikulu linapereka chigamulochi pa 4 September 2014. Onani nkhani ya m’Chingelezi yakuti, “Kyrgyzstan’s Highest Court Upholds Religious Freedom for Jehovah’s Witnesses.”