Posachedwapa khoti lalikulu la ku Kyrgyzstan lizenga milandu iwiri yokhudza ufulu wachipembedzo, wosonkhana ndiponso wonena maganizo ako.

  • 15 February 2016. A Mboni za Yehova anachita apilo kukhoti lalikulu ataona kuti komiti yoona za zinthu zokhudza zipembedzo m’dzikoli inakana kulemba m’kaundula mabungwe 4 a Mboni. Komitiyi inanyalanyaza zimene khoti lalikulu linagamula pa nkhaniyi pa September 4, 2014.

  • 24 February 2016. Loya wa boma wamumzinda wa Osh anachita apilo chigamulo chonena kuti Oksana Koriakina ndi mayi ake a Nadezhda Sergienko alibe mlandu uliwonse. A Mboni za Yehova sakusangalala kuti boma lalola zoti loya wamkulu wa boma adzaimire loya wa boma wamumzinda wa Osh pa apiloyi. Zili choncho chifukwa chakuti zigamulo za makhoti ang’onoang’ono zinasonyeza kale kuti ufulu wa Oksana ndi a Nadezhda unaphwanyidwa.