Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

9 FEBRUARY, 2017
KAZAKHSTAN

Khoti la ku Kazakhstan Lalamula Kuti a Mboni Asungidwe M’ndende Ngakhale Kuti Mlandu Wawo Sunazengedwe

Khoti la ku Kazakhstan Lalamula Kuti a Mboni Asungidwe M’ndende Ngakhale Kuti Mlandu Wawo Sunazengedwe

Pa 30 January, 2017, khoti la mumzinda wa Astana linakana ma apilo oti limasule a Teymur Akhmedov komanso a Asaf Guliyev omwe anamangidwa asanawazenge mlandu. Iwo anamangidwa pa 18 January chifukwa cholalikira gulu lina la amuna amene ananamizira kuti ali ndi chidwi ndi zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa. A Mboniwo anaimbidwa mlandu “woyambitsa mkangano pankhani za chipembedzo” komanso “kuchititsa anthu kuganiza kuti chipembedzo chawo n’chapamwamba.” Khotilo silinapereke umboni uliwonse wosonyeza kuti a Mboniwo ankayeneradi kumangidwa.

Khoti lagamula kuti anthuwa amangidwe ndipo sakuloledwa kupanga apilo. Ngakhale kuti mlandu wawo sunazengedwe, a Teymur ndi a Asaf akuyenera kukhalabe m’ndende mpaka ntchito yofufuza mlanduwu itatha. Ngati angapezeke olakwa, akhoza kukhala m’ndende zaka 5 kapena10.