Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JANUARY 26, 2017
KAZAKHSTAN

Akuluakulu a Boma a ku Kazakhstan Anamanga a Mboni pa Mlandu Wabodza

Akuluakulu a Boma a ku Kazakhstan Anamanga a Mboni pa Mlandu Wabodza

Pa 18 January 2017, komiti yoona za chitetezo m’dziko la Kazakhstan inamanga Teymur Akhmedov ndi Asaf Guliyev chifukwa cholankhula ndi anthu ena zokhudza zikhulupiriro zawo. M’mwezi wa May ndiponso wa June 2016, anthu 7, omwe anati anakafuna kudziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira, anaitana Teymur ndi Asaf kuti akakambirane nawo kunyumba ina yalendi. Komanso pa nthawi ina anthuwo anakumana ndi Teymur ndi Asaf kunyumba zawo. A Mboniwa sankadziwa kuti anthuwa ankajambula vidiyo ya zimene ankakambiranazo.

Chifukwa chokambirana ndi anthuwa mwamtendere za chipembedzo chawo, Teymur ndi Asaf anaimbidwa mlandu “woyambitsa chisokonezo pa nkhani ya chipembedzo” komanso ‘wouza anthu kuti chipembedzo chawo ndi chabwino kwambiri.’ Panopa a Mboniwa ali m’ndende kwa masiku 60 podikira kuti mlandu wawo udzazengedwe. Akawapeza kuti ndi olakwa kukhoti akhoza kuweruzidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka 5 kapena 10.

Teymur ali ndi zaka 61 ndipo ali ndi matenda aakulu pomwe Asaf ali ndi zaka 43. Onsewa ali pa banja. Maloya awo amaganiza kuti khoti lidzamva apilo yawo pa mlungu woyambira 23 January 2017.