Mu April 2012, mwana wina wazaka 7 dzina lake Vivienne Falcone, anakapereka kalata yochokera kwa makolo ake kwa woyang’anira sukulu imene ankaphunzira, yopempha kuti amulole kuti asabwere ku sukulu kwa tsiku limodzi. Banja la mtsikanayu linakonza zoti lipite kumsonkhano wapachaka wa Mboni za Yehova wa masiku atatu womwe unkachitikira mu mzinda wa Mainz. Akuluakulu a sukuluyo anakana zoti Vivienne adzajombe kusukulu Lachisanu lomwe msonkhanowo unkayamba. Komabe, makolo a mtsikanayo anaona kuti ndi bwino kuti apite ndi mwana wawoyo ku msonkhano ngakhale kuti kusukulu sanamulole. Makolo a Vivienne anakadandaula za nkhaniyi ku bungwe loyang’anira za maphunziro m’dzikolo. M’malo moona msonkhanowo ngati holide yachipembedzo, bungwelo linalamula makolo a Vivienne kuti apereke chindapusa.

Zimene bungwelo linanena zikanaika makolo a Vivienne m’mavuto chifukwa chakuti mogwirizana ndi malamulo a ku Germany, kujomba ku sukulu popanda chilolezo ndi kuphwanya lamulo loti makolo ali udindo wotumiza ana awo ku sukulu. Munthu akhoza kulipira chindapusa kapena kukakhala kundende kumene, chifukwa cha mlanduwu. Komabe, makolo a Vivienne anaona kuti kuletsa mwana wawo kupita ku msonkhano kukuphwanya ufulu wawo wopembedza komanso wolera mwana wawo mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.

Nkhani ya Ufulu wa Maholide Achipembedzo Inalowa M’khoti

Makolo a Vivienne, omwe ndi a Stefano komanso a Elisa, anakadandaula ku khoti chifukwa cha zimene bungwe loyang’anira maphunziro linachita. Iwo ananena kuti kupezeka pa msonkhano tsiku lonse kumawapatsa mwayi wopembedza Mulungu monga banja ndipo izi zimalimbitsa chikhulupiriro chawo. Iwo anati: “Misonkhano yachigawo imachitika kamodzi pachaka ndipo imakhala nthawi yapadera kwambiri pa kulambira kwathu.” * Khotilo linagamula nkhaniyo mokomera makolo a Vivienne ndipo linanena kuti misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova imakhala maholide achipembedzo. Koma bungwe loyang’anira maphunziro linachita apilo nkhaniyi ndipo linanena kuti misonkhano ya Mboni za Yehova si maholide a chipembedzo chifukwa chakuti ndi zochitika zachikondwerero, osati masiku apadera omwe amakhala opatulika, monga Khirisimasi, Isitala kapena maholide ena.

Pa 27July , 2015, Khoti Lalikulu Kwambiri la ku Hesse linapereka chigamulo chogwirizana ndi chimene khoti laling’ono lija linapereka. Khoti lalikululo linanena kuti tanthauzo la holide ya chipembedzo likudalira pa mmene chipembedzocho chimaonera nkhaniyo. Khotilo linaona kuti pali kusiyana pakati pa nkhani za chipembedzo ndi nkhani za boma ndipo linati: “Boma litati lizilowerera nkhani za chipembedzo, ndiye kuti likhoza kuphwanya ufulu umene malamulo oyendetsera dziko la Germany amapereka ku zipembedzo komanso mabungwe omwe ali ndi mfundo zina zake zomwe amazikhulupirira, wochita zinthu moipa pawokha.” Boma lili ndi “udindo woonetsetsa kuti silikulowerera maganizo a anthu komanso mfundo zimene zipembedzo zimayendera.”

Khoti lalikululo linatchulanso za webusaiti ya Mboni za Yehova, imene imafotokoza kuti a Mboni amaona misonkhano yawo ikuluikulu monga maholide achipembedzo. Khotilo linanenanso kuti zimene bungwe loyang’anira maphunziro linachita pokana pempho la makolo a Vivienne loti mwana wawo amulole kupita ku msonkhano, ndi “kusaganizira ufulu wopembedza womwe mwana ali nawo. . . komanso ufulu wa makolo. . . wophunzitsa ana awo zokhudza chipembedzo chawo komanso zimene amakhulupirira.” Pomaliza khotilo linanena kuti zimene bungwe loyang’anira maphunzirolo linachita “n’zosemphana ndi zomwe boma likuyenera kuchita posalowerera mu nkhani za chipembedzo.”

“Kukapezeka pa mwambo waung’ono wa mapemphero ndi chifukwa chokwanira chochititsa kuti mwana aloledwe kuchoka ku sukulu.”—Khoti Lalikulu la ku Hesse

Maphunziro Othandiza M’mbali Zosiyanasiyana

Pambuyo pa chigamulochi, makolo a Vivienne anati: “Monga a Mboni za Yehova, timaona kuti maphunziro ndi ofunika kwa ife, ndipo timayesetsa kulimbikitsa ana athu kuti azikonda kuphunzira. Koma timaonanso kuti zimene timaphunzira ku misonkhano yathu zimathandiza kwambiri ana athu kuti azikonda zinthu zauzimu ndi kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, zomwe zimawathandiza kuti azikonda ndi kuchita zinthu moganizira anthu ena komanso kukhala anthu abwino. Tikuyamikira kwambiri chigamulo chimene makhotiwa apereka.”

A Armin Pikl, omwe ndi loya wa makolo a Vivienne, ananena kuti: “Chigamulo chimenechi chikusonyeza kuti misonkhano ya Mboni za Yehova ndi yopatulika ndipo chikutsimikizira kuti makolo ali ndi ufulu wophunzitsa ana awo zinthu zimene amakhulupirira. Ana a sukulu a Mboni za Yehova apindula chifukwa tsopano azikhala ndi mwayi wopezeka pa misonkhano yothandiza kwambiri imeneyi chaka chili chonse. Ndikukhulupirira kuti chigamulochi chithandizanso akuluakulu a zamalamulo m’mayiko ena akamaweruza nkhani ngati imeneyi.”

^ ndime 5 Misonkhano yachigawo ndi zochitika zapadera zauzimu zimene a Mboni za Yehova amakhala nazo padziko lonse chaka chilichonse. Misonkhanoyi imakhala ya masiku atatu ndipo imathandiza ana ndi akuluakulu omwe mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo.