Pitani ku nkhani yake

A Mboni za Yehova akulalikira pafupi ndi mlatho wotchedwa Bridge of Peace womwe uli mu mzinda wa Tbilisi.

21 FEBRUARY, 2017
GEORGIA

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lathandiza Kuti a Mboni za Yehova Akhale ndi Ufulu Wopembedza ku Georgia

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lathandiza Kuti a Mboni za Yehova Akhale ndi Ufulu Wopembedza ku Georgia

Zaka zochepa zapitazo, a Mboni za Yehova m’dziko la Georgia analibe ufulu wopembedza ngati umene ali nawo pano. Panopa boma limalola kuti a Mboni za Yehova azipembedza mwaufulu. Koma mmenemu si mmene zinthu zinalili kuyambira mu 1999 mpaka 2003. Pa nthawiyi boma linkalekerera magulu azipembedzo zankhanza kuti azizunza a Mboni ndipo silinkaimba mlandu magulu oipawa.

Imodzi mwa makalata amene a Mboni analemba inali yokhudza mlandu wa a Tsartsidze ndi anthu ena (Case of Tsartsidze and Others v. Georgia) ndipo inanena nthawi zitatu zimene a Mboni anachitiridwa nkhanza ku Georgia kuyambira mu 2000 mpaka 2001. Pa nthawiyo gulu la anthu linawachitira nkhanza , kusokoneza misonkhano yawo, kuwawonongera katundu, kuwamenya komanso apolisi ankawayankhula zachipongwe.

Pa 17 January, 2017, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linalengeza chigamulo chake pamlanduwu ndipo khotilo linapeza kuti ufulu wa a Mboni unaphwanyidwa. Khotili linapeza kuti apolisi ku Georgia anazunza nawo a Mboni kapenanso analephera kuwateteza. Linapezanso kuti makhoti komanso oweruza milandu a m’dzikomo analephera kuteteza a Mboni ndipo anachita zinthu mokondera komanso sanafufuze mokwanira nkhaniyo.

Chigamulo Chachitatu Chodzudzula Boma Chifukwa Cholimbikitsa Nkhanza

Chimenechi chinali chigamulo chachitatu cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe chodzudzula boma la Georgia chifukwa cha nkhanza zimene a Mboni anachitiridwa m’dziko lonselo kuyambira mu 1999 mpaka 2003. M’zigamulo zake zonse zitatu, khotilo linapeza kuti boma la Georgia linaphwanya mfundo za mu Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Europe chifukwa cholephera kuteteza ufulu wolambira wa Mboni za Yehova komanso chifukwa chowachitira za tsankho.

Pofotokoza mmene zinthu zinalili panthawiyo ku Georgia, khotili linati: “Akuluakulu a boma la Georgia anachititsa kuti a Mboni azunzidwe m’dziko lonselo chifukwa cholekerera anthu ena kuti aziwachitira nkhanza. Ena mwa anthuwa anali nthumwi za boma zomwenso zinkazunza a Mboni kapena kulimbikitsa anthu ena kuti azizunza a Mboniwo.”

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Linapeza Kuti Boma la Georgia Linaphwanya Malamulo Komanso Ufulu Wopembedza

Pozenga mlandu wa a Tsartsidze khotili linaunika nkhanza zimene zinachitika maulendo atatu ndipo linapeza kuti a Mboni anazunzidwa ndi apolisi kapenanso kuti apolisiwo anathandiza anthu amene ankazunza a Mboniwo.

  • Pa 2 September, 2000, apolisi mu mzinda wa Kutaisi anamanga a Dzamukov. Anawalanda mabuku amene anali nawo, kuwanyoza komanso kuwamenya. Tsiku lotsatira, wapolisi anamenya a Gabunia pamimba komanso anang’amba mabuku amene ananyamula.

  • Pa 26 October, 2000, apolisi mu mzinda wa Marneuli anasokoneza mwachipongwe msonkhano wa a Mboni komanso analanda mabuku awo. Kenako anagwira a Mikirtumov omwe panthawiyo ankakamba nkhani, ndi a Aliev omwe ndi eniake a nyumba imene ankachitiramo msonkhanowo. Kenako apolisiwo anatenga a Mikirtumov pagalimoto mowakakamiza n’kuchoka nawo mu mzindawo ndipo anawalamula kuti asadzabwererenso. Analamulanso a Aliev kuti asadzachitenso misonkhano ya Mboni za Yehova m’nyumba yawo.

  • Pa 27 March, 2001, gulu la anthu achiwawa a chipembedzo cha Orthodox mu mzinda wa Rustavi, linafika pa nyumba ya a Gogelashvili misonkhano ili mkati. Iwo ananyoza anthu amene anali pamalowo ndipo kuwathamangitsa. Gululo linalanda mabuku a Mboni ndipo tsiku lotsatira anawaotchera pafupi ndi msika anthu akuona. Apolisi sanafune kuthandiza a Mboniwo.

Pa nthawi zonsezi a Mboni ankakadandaula ku makhoti koma sankathandizidwa. Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapeza kuti oweruza milandu a m’dziko la Georgia ankachita zinthu mokondera apolisi ndipo sankafuna kugwiritsa ntchito umboni umene a Mboniwo ankapereka. Pofotokoza zimene oweruza milandu a ku Georgia ankachita pa nkhanizi, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linanena kuti:

Zimene oweruzawa ankachita posafufuza mokwanira, kukondera poweruza mlandu ndiponso kumangokhulupirira zonse zimene apolisi ankanena, komanso kukana kumvetsera mbali ya odandaula, kunasonyeza kuti oweruza milandu ankagwirizana ndi zimene anthu ankhanzawa ankachitira a Mboni.

Gawo 9 la Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Europe limafotokoza za ufulu wopembedza umene anthu ali nawo, pomwe gawo 14 limaletsa kuchitira ena zinthu mwa tsankho. Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapeza kuti a Mboni anawaphwanyira ufulu wawo wopembedza komanso anawachitira za tsankho. Chifukwa cha zimenezi, khotilo linalamula kuti dziko la Georgia lipereke kwa a Mboni ndalama zokwana madola 11,840 a ku America komanso lilipire ndalama zokwana madola 10,762 zomwe zinagwiritsidwa ntchito pa mlanduwo.

Kodi Chigamulochi Chithandizanso Mayiko a Russia ndi Azerbaijan Kulemekeza Ufulu Wopembedza wa a Mboni?

Pomaliza kupereka chigamulo chake, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linabwerezanso zigamulo zomwe linapereka pa mlandu wokhudza mpingo wa Mboni za Yehova wa Gldani ndi a Begheluri a ku Georgia komanso wa a Kuznetsov ndi a Krupko a ku Russia. Pang’ono ndi pang’ono, boma la Georgia lakhala likutsatira zimene khotili linagamula m’mbuyomu ndipo a Mboni za Yehova m’dzikoli akuyamikira chifukwa tsopano ndi otetezedwa, zomwe zimawapangitsa kuti azitha kusonkhana komanso kuuzako ena zimene amakhulupirira mwaufulu ndi mopanda mantha.

Loya woona za ufulu wa anthu m’mayiko osiyanasiyana dzina lake André Carbonneau, yemwe anatenga nawo mbali pamene makhoti a ku Georgia ankazenga milandu ya a Mboni, komanso pamene kalata yopita ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe inkalembedwa, ananena kuti: “Popereka chigamulo chabwino kwambiri chimenechi, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe lasonyezeratu kuti silidzalola mayiko omwe ndi mamembala ake kuti aziphwanya ufulu wopembedza wa nzika zake. A Mboni za Yehova ndi osangalala chifukwa choti boma la Georgia likuyesetsa kugwiritsa ntchito zigamulo zomwe zinaperekedwa n’cholinga choti azitha kulambira mwaufulu. Tikukhulupirira kuti mayiko enanso omwe ali m’Bungwe la Mayiko a ku Europe monga Russia aona zomwe dziko la Georgia likuchita.”

Chigamulo chomwe Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe lapereka posachedwapa, chikuteteza maufulu ofunika kwambiri a anthu omwe ndi kusonkhana pamodzi n’cholinga cholambira Mulungu komanso kuuza ena zimene amakhulupirira mwamtendere. A Mboni za Yehova padziko lonse akukhulupirira kuti chigamulochi chithandizanso pa milandu yokhudza a Mboni za Yehova ku Russia ndi Azerbaijan.