Pitani ku nkhani yake

FRANCE

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku France

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku France

Chipembedzo cha Mboni za Yehova chinakhala chovomerezeka ndi boma ku France mu 1906, ndipo tingati ali ndi ufulu wolambira. Komabe, chapakati pa zaka za m’ma 1990 lipoti lochokera kunyumba ya malamulo la mutu wakuti “Timagulu Toukira ku France,” linaika a Mboni za Yehova pa m’ndandanda wa timagulu tomwe ankati n’toopsa. Ngakhale kuti zimenezi sizinakhudze malamulo, lipotilo linagwiritsidwa ntchito polimbana ndi a Mboni, zomwe zinachititsa kuti anthu ayambe kusalemekeza komanso kusala a Mboni.

Chinthu choopsa kwambiri chomwe boma linachita ndi kukweza kwambiri msonkho pa katundu yemwe likulu la a Mboni m’dzikolo linkalandira n’cholinga chofuna kuti ndalama zoyendetsera likululo zithe. A Mboni atamenyera nkhondo ufulu wawo m’makhoti kwa zaka 16, pa 30 June, 2011, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linagamula kuti boma la France linaphwanyira a Mboni ufulu wawo wopembedza. A Mboni za Yehova ku France analimbana ndi mchitidwe wa tsankho womwe ankawachitira, anamenyera nkhondo pa nkhani yowakaniza chilolezo kuti azitha kumanga zinthu zosiyanasiyana ndiponso kuti azitha kumakalalikira m’malo osiyanasiyana monga kundende, komanso kuwakaniza kuchita lendi maholo kuti achitiremo misonkhano yawo.

Zomwe boma la France lakhala likuchitira a Mboni za Yehova zimachititsa kuti anthu aziwakayikira. Izi zili choncho ngakhale kuti Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapereka chigamulo chokomera a Mboni komanso a Mboni awina milandu yambiri m’makhoti a ku France. Chifukwa cha zimenezi, anthu akupitirizabe kuchitira a Mboni nkhanza, kuwazunza, komanso kuthyola malo awo olambirira n’kubamo zinthu.