Dziko la Eritrea likumanga a Mboni za Yehova komanso anthu a zipembedzo zina zing’onozing’ono popanda kuzenga mlandu kapenanso zifukwa zomveka. Azibambo ndi azimayi a Mboni kuphatikizapo ana ndi achikulire omwe akumangidwa chifukwa chochita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo kapena pa zifukwa zosadziwika bwino. Pomwe anyamata akumangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

Dziko la Eritrea litalandira ufulu wodzilamulira mu 1993, ufulu wa a Mboni za Yehova unayamba kuphwanyidwa. Pa October 25, 1994, pulezidenti Afewerki analamula kuti a Mboni za Yehova ndi osaloledwa kukhala nzika za dzikoli chifukwa anakana kuvota mu 1993 komanso amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Kuyambira nthawi imeneyo, asilikali a dziko la Eritrea akhala akumanga komanso kuzunza a Mboni za Yehova n’cholinga choti asiye zimene amakhulupirira.

Akukhala Mozunzika Kundende Popanda Kuwauza Nthawi Yotuluka

Azibambo atatu a Mboni omwe ndi a Paulos Eyassu, a Isaac Mogos, ndi a Negede Teklemariam akhala ali m’ndende kuyambira pa September 24, 1994 chifukwa choti anakana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Akaidi ena a Mboni anatsekeredwa m’makontena achitsulo pomwe ena anatsekeredwa m’nyumba zomangidwa ndi miyala kapena zitsulo ndipo hafu ya nyumba iliyonse ndi yokwiririka pansi. A Misghina Gebretinsae, a zaka 62, anamwalira mu July 2011 chifukwa cha kutentha pa nthawi imene anatsekeredwa m’ndende ina yachitsulo yomwe hafu yake inakwiriridwa pansi. Ndendeyi amaitcha Meitir. A Yohannes Haile, a zaka 68, anamwalira pa August 16, 2012 atakhala zaka pafupifupi 4 m’ndende yotchedwa Meitir. Nawonso anafa mozunzika ngati mmene anafera a Misghina Gebretinsae. Akaidi a Mboni ochepa anatulutsidwa m’ndende ya Meitir atadwala mwakayakaya.

Amene Amangidwa Posachedwapa

Pa April 14, 2014, tsiku lomwe a Mboni za Yehova padziko lonse ankachita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu, akuluakulu a dziko la Eritrea anamanga anthu 90 omwe ankachita mwambowu. Anamanga amuna, akazi ngakhale ana kuyambira a miyezi 16 mpaka anthu a zaka zoposa 85. Pa April 27, 2014, akuluakulu a dziko la Eritrea anamanga anthu 31 amene anasonkhana n’kumaphunzira Baibulo. Panopa sitikudziwa zambiri zokhudza zifukwa zimene amangidwira, anthu amene adakali m’ndende pakali pano komanso mmene akukhalira kundendeko.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. December 12, 2014

  A Mboni za Yehova 64 anamangidwa popanda kuimbidwa mlandu uliwonse.

 2. July 25, 2014

  Ambiri mwa anthu amene anamangidwa pa April 14 anatulutsidwa koma 20 mwa anthu amene anamangidwa pa April 27 sanatulutsidwebe. A Mboni okwana 73 anali adakali m’ndende.

 3. April 27, 2014

  A Mboni 31 anamangidwa atasonkhana n’kumaphunzira Baibulo.

 4. April 14, 2014

  A Mboni oposa 90 anamangidwa akuchita mwambo wa pachaka wokumbukira imfa ya Yesu Khristu.

 5. November 2013

  A Mboni 52 anamangidwa ndipo ankakhala mozunzika kwambiri kundende.

 6. August 16, 2012

  A Yohannes Haile anamwalira ali ndi zaka 68. Anamwalirira kundende chifukwa chokhala mozunzika kwambiri.

 7. July 2011

  A Misghina Gebretinsae anamwalira ali ndi zaka 62. Anamwalirira kundende chifukwa chokhala mozunzika kwambiri.

 8. June 28, 2009

  Akuluakulu a boma analowa m’nyumba ya wa Mboni akuchita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo ndipo anamanga anthu onse 23 omwe anali m’nyumbamo. Anthuwa anali a zaka kuyambira ziwiri mpaka 80. Chiwerengero cha a Mboni amene anali m’ndende chinakwera mpaka kufika 69.

 9. April 28, 2009

  Akuluakulu a boma anasamutsa a Mboni za Yehova onse, kungosiya mmodzi, omwe anatsekeredwa kusiteshoni ya apolisi n’kuwapititsa kundende ya Meitir.

 10. July 8, 2008

  Akuluakulu a boma anayamba kuyenda m’nyumba ndi m’malo ogwirira ntchito kumasakasaka a Mboni ndipo anamanga a Mboni 24. Ambiri mwa anthuwa anali oti ndi amene amagwira ntchito kuti azisamalira mabanja awo.

 11. May 2002

  Boma linatseka zipembedzo zonse zomwe sizili m’gulu la zipembedzo 4 zovomerezeka ndi boma.

 12. October 25, 1994

  Pulezidenti analamula kuti a Mboni za Yehova si nzika zovomerezeka za dzikolo ndipo analandidwa ufulu pa zinthu zosiyanasiyana.

 13. September 24, 1994

  A Paulos Eyassu, a Isaac Mogos, ndi a Negede Teklemariam anamangidwa popanda kuimbidwa mlandu kapena kuuzidwa zimene alakwa ndipo adakali m’ndende mpaka pano.

 14. M’ma 1940

  A Mboni za Yehova anayamba kupezeka m’dziko la Eritrea.