Pitani ku nkhani yake

A Habtemichael Tesfamariam ndi akazi awo a Leterberhan Bezabih. Pa nthawiyi n’kuti a Tesfamariam asanamangidwe

APRIL 25, 2018
ERITREA

A Mboni za Yehova Awiri Achikulire Anafera M’ndende ku Eritrea

A Mboni za Yehova Awiri Achikulire Anafera M’ndende ku Eritrea

Kumayambiriro kwa chaka cha 2018, a Mboni za Yehova awiri omwe mayina awo ndi a Habtemichael Tesfamariam ndi a Habtemichael Mekonen, anafera m’ndende ya Mai Serwa yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Asmara. A Mboniwa anamangidwa ndi kuikidwa m’ndende mu 2008 chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo anakhala mozunzika m’ndendemo kwa zaka pafupifupi 10.

A Tesfamariam anafa mwadzidzidzi pa 3 January, 2018, m’ndende ya Mai Serwa ali ndi zaka 76. Akaidi anzawo amakhulupirira kuti bambowa anadwala matenda opha ziwalo. A Tesfamariam anabadwira ku Adi Yakulu, Mendefera, m’dziko la Eritrea mu 1942. Iwo anakhala a Mboni za Yehova mu 1970 ndipo anakana kuchita zinthu zosemphana ndi zimene amakhulupirira ngakhale kuti anaikidwa m’ndende mopanda chilungamo komanso kuzunzidwa. Iwo asiya mkazi dzina lake Leterberhan Bezabih, ana aamuna 4, ndi aakazi atatu.

A Mekonen anafa pa 6 March, 2018, m’ndende ya Mai Serwa ali ndi zaka 77. Akaidi anzawo amakhulupirira kuti bambowa anafa chifukwa cha vuto la impso. Iwo anabadwa mu1940 kum’mwera kwa dziko la Eritrea m’mudzi wotchedwa Kudo Felasi. A Mekonen anakhala a Mboni zaka zoposa 55 zapitazo, ndipo mofanana ndi a Tesfamariam, anakana kuchita zinthu zosemphana ndi zimene amakhulupirira ngakhale kuti anaikidwa m’ndende popanda chifukwa komanso anazunzidwa. Iwo asiya mkazi dzina lake Mihret Ellias, mwana wamwamuna komanso wamkazi.

Anamangidwa Mopanda Chilungamo Komanso Kuzunzidwa

Mu July 2008, a Mekonen anamangidwa popanda chifukwa ndipo panthawiyi n’kuti ali kunyumba kwawo. Nawonso a Tesfamariam anali ali kwawo pamene ankamangidwa mu August 2008. Kenako, anaikidwa m’ndende yoipa kwambiri ya Meitir yomwe ili m’chipululu kumpoto kwa mzinda wa Asmara ndipo anakhala m’ndendemo mozunzika kwambiri komanso anapirira moyo wovuta kwambiri. Pofuna kupereka chilango chapadera kwa akaidi omwe ndi a Mboni, kuyambira mu October 2011 mpaka August 2012, akuluakulu a ndendeyo anaika a Mboniwo m’nyumba ina yomwe hafu yake ili pansi panthaka. Akaidiwo anazunzika chifukwa cha kutentha komanso kusowa kwa chakudya kapena madzi okwanira. Zimenezi zinachititsa kuti ena adwale kwa nthawi yaitali.

Mu 2017, akuluakulu andende anasamutsa a Mboni omwe anali m’ndende ya Meitir n’kuwaika m’ndende ya Mai Serwa ndipo kumeneko amalola kuti achibale awo aziwabweretsera chakudya komanso kulandira chithandizo chamankhwala akadwala kwambiri. A Mboniwo anagwirizana ndi zoti awasamutsire ku ndende yabwinoko, koma mavuto omwe a Tesfamariam ndi a Mekonen ankakumana nawo chifukwa chozunzidwa ku ndende ya Meitir sanatheretu.

A Habtemichael Mekonen ndi akazi awo a Mihret Ellias. Apa n’kuti a Mekonen asanamangidwe

A Tesfamariam ndi a Mekonen si a Mboni oyamba kufera m’ndende kapena kufa atangotulutsidwa kumene m’ndende ku Eritrea. Palinso a Mboni ena awiri amene anafera m’ndende komanso ena atatu amene anafa atangotulutsidwa kumene m’ndende chifukwa chokhala moyo wovutika kwambiri kundende komanso kuzunzidwa. A Mboni osachepera 7 omwe anatulutsidwa m’ndende zaka zingapo zapitazo, amavutikabe kwambiri ndi matenda amene anayamba kudwala chifukwa cha zimene anakumana nazo ali m’ndende. Ku Eritrea, kuli a Mboni 53 omwe akanali m’ndende chifukwa cha zimene amakhulupirira, ndipo mmodzi mwa iwo ndi a Tareke omwe ndi mchimwene wawo wa a Tesfamariam.

Kuzunza Anthu ndi “Mlandu Wophwanya Ufulu wa Anthu”

Nthambi ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inakhazikitsa gulu loti lifufuze mmene dziko la Eritrea likuchitira pa nkhani yokhudza ufulu wa anthu. Nthambiyi inachita zimenezi n’cholinga chofuna kudziwa ngati dziko la Eritrea likuphwanya ufulu wa anthu kapena ayi, ndipo nthambiyi inatulutsa zomwe gululo linapeza pa 8 June, 2016.

Gululi linapempha boma la Eritrea kuti liyambe “kulemekeza ufulu wachipembedzo kapena wa zinthu zomwe munthu amakhulupirira.” Linapemphanso kuti bomalo “lisiye kumanga anthu popanda chifukwa, komanso kumanga anthu chifukwa cha zimene amakhulupirira, makamaka anthu omwe ali m’zipembedzo zinazake monga a Mboni za Yehova, . . . komanso kuti limasule mwamsanga anthu omwe anamangidwa mosagwirizana ndi malamulo komanso popanda chifukwa, ndipo anthuwo sakuyenera kuchita zinazake kaye kuti atulutsidwe.” Gululo linamaliza lipoti lake ponena kuti kuzunza anthu kumene boma la Eritrea likuchita chifukwa cha zimene anthuwo amakhulupirira, ndi “mlandu wophwanya ufulu wa anthu.”

A Mboni za Yehova akukhulupirira kuti kufa kwa a Tesfamariam komanso a Mekonen kudziwika kwa anthu a m’mayiko ena, komanso kuti zimene zachitikazi zipangitsa akuluakulu ena a boma la Eritrea a mtima wabwino kuti achitepo kanthu m’malo mwa anthu omwe anatsekeredwa m’ndende mopanda chilungamo chifukwa cha zimene amakhulupirira.