Pitani ku nkhani yake

DEMOCRATIC REPUBLIC OF CONGO

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Democratic Republic of Congo

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Democratic Republic of Congo

A Mboni za Yehova akhala akupezeka ku Democratic Republic of Congo kuyambira cha m’ma 1940. Mbiri yawo yonse imasonyeza kuti akhala akuvutika ndi nkhondo, boma lakhala likuletsa ntchito yawo, komanso anthu azipembedzo zina akhala akuwachitira zankhanza.

Boma linasiya kutsutsa a Mboni mu 1993 pa nthawi imene Khoti Lalikulu Kwambiri linanena kuti a Mboni asaletsedwenso ntchito zawo. Panopa tingati a Mboni za Yehova ali ndi ufulu wochita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo popanda kusokonezedwa ndi boma. Komabe, magulu ena achipembedzo akupitirizabe kuopseza kapena kuzunza a Mboni. Anthu a m’gulu lachipembedzo chotchedwa Kimbilikiti akhala akuzembetsa komanso kuchitira a Mboni ambiri nkhanza zoopsa. Nthawi zambiri akuluakulu a m’madera omwe mumachitika zoopsazi saimba mlandu anthu amenewa ndipo ena mwa akuluakuluwa ali m’chipembedzo cha Kimbilikiti. Oimira Mboni za Yehova anapanga apilo za nkhanizi ku makhoti aakulu chifukwa choti chilungamo sichinachitike.

Komanso, masukulu ambiri ku DRC amathandizidwa ndi mabungwe azipembedzo. Zotsatirapo zake ndi zakuti masukuluwa anathamangitsa ana asukulu omwe ndi a Mboni chifukwa chokana kupezeka nawo komanso kuchita nawo zinthu zachipembedzo pa sukulu. Mu 2013, Nduna ya Zamaphunziro inalamula kuti anthu m’masukulu onse a m’dzikolo asiye kudana chifukwa chosiyana zipembedzo. Potsatira lamuloli kuphatikizanso lamulo lina latsopano lokhudza maphunziro, ana omwe anachotsedwa sukulu abwezeretsedwa sukulu komanso ana asukulu omwe anawakaniza madipuloma awo awapatsa.