Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JUNE 14, 2016
BULGARIA

Bungwe Loona Zamalamulo ku Bulgaria Ladzudzula Mchitidwe wa Tsankho Limene Limachitika Chifukwa Chosiyana Zipembedzo

Bungwe Loona Zamalamulo ku Bulgaria Ladzudzula Mchitidwe wa Tsankho Limene Limachitika Chifukwa Chosiyana Zipembedzo

A Mboni za Yehova ku Bulgaria apambana pa nkhani ina yomwe ikupatsa anthu ufulu woyankhula komanso kuteteza anthuwo ndi mabungwe ku tsankho limene limachitika chifukwa chosiyana zipembedzo. Bungwe lina lolimbana ndi tsankho m’dzikolo linapeza kuti wailesi youlutsa nkhani pa TV ya SKAT komanso atolankhani ake awiri, anafalitsa mwadala nkhani zabodza zokhudza a Mboni za Yehova zimene zinachititsa kuti anthu azichitira chipongwe a Mboniwo. Bungwelo linanena kuti zimene wailesiyo inachita ndi “zosavomerezeka.”

Nkhani Zimene Zinaulutsidwa pa TV Zinayambitsa Chidani Komanso Chiwawa

Masiteshoni a TV m’dziko la Bulgaria nthawi zina amaulutsa ma pulogalamu amene amakhala ndi nkhani zabodza zomwe cholinga chake ndi kuipitsa mbiri ya a Mboni za Yehova. Makamaka atolankhani a siteshoni ya SKAT ankaulutsa nkhani zabodza zokhudza a Mboni zimene zinkachititsa anthu kukhulupirira kuti a Mboniwo amachita zinthu zambiri zoopsa. Nkhani zoterezi zakhala zikufalitsidwa m’dziko lonselo komanso kuikidwa pa intaneti.

Mapulogalamu amenewa achititsa anthu kuti azidana ndi a Mboni za Yehova komanso kuwachitira nkhanza. Mu pulogalamu imene inaulutsidwa mu May 2011, siteshoni ya TV ya SKAT inanena kuti zimene anthu anachita poukira mwankhanza a Mboni za Yehova komanso Nyumba yawo ya Ufumu mu mzinda wa Burgas, zinali zoyenera. A Mboniwo anasonkhana kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu koma kenako kunabwera gulu la anthu amene analowa mu Nyumba ya Ufumuyo ndipo linamenya mwankhanza anthu ambiri amene ankachita nawo mwambowo. Anthu 5 anavulala ndipo anawatengera kuchipatala. Siteshoni ya SKAT inalimbikitsa anthu kuti azimenya a Mboni ndipo mapulogalamu otsatira amene siteshoniyi inaulutsa ananena motsindika kuti anthu sankalakwa pomenya a Mboni. *

Siteshoniyi itanena zimenezi, a Mboni anavutitsidwa kwambiri chifukwa cha zinthu zankhanza zimene anthu anawachitira ndipo Nyumba za Ufumu zambiri zinawonongedwa. M’zigawo zina, akuluakulu oyang’anira matauni anakhazikitsa malamulo omwe cholinga chake chinali kuletsa zimene a Mboni amachita.

A Mboni akuchita misonkhano mu Nyumba ya Ufumu ku Burgas

Bungwe Lolimbana ndi Tsankho Lalamula Amene Anafalitsa Nkhani Zabodzazo Kuti Alipire Chindapusa

Mu February 2012, a Mboni za Yehova anapereka dandaulo lawo ku bungwe lolimbana ndi mchitidwe wa tsankho pa mapulogalamu 6 amene siteshoni ya SKAT inaulutsa mu 2010 komanso mu 2011. A Mboni anapereka umboni wosonyeza kuti siteshoniyo inagwiritsa ntchito mawu a tsankho komanso kuti kuulutsidwa kwa mapulogalamu amenewa kunachititsa kuti a Mboniwo azizunzidwa ndi kunyozedwa. Anafotokozanso kuti mapulogalamuwo anachititsa kuti iwo azisalidwa kwambiri.

Pa 25 January, 2016, bungwe lolimbana ndi tsankholo linapereka chigamulo chimene chinakomera a Mboni. Linapezanso kuti siteshoni ya SKAT komanso atolankhani ake awiri anachitira nkhanza a Mboniwo pofalitsa nkhani zabodza komanso zopanda umboni. Bungwelo linanena kuti mapulogalamu 6 amene siteshoniyo inaulutsa, kwenikweni linali tsankho lolimbana ndi chipembedzo cha Mboni za Yehova. Linanenanso kuti zimene siteshoniyo ndi atolankhani ake anachita n’zosagwirizana ndi malamulo a ntchito ya utolankhani.

Popereka chigamulo chake, bungwelo linanena kuti “a Mboni za Yehova onse m’dzikolo achitiridwa zinthu zimene n’zosayenera komanso zosemphana ndi malamulo, ndipo kuchita zimenezi ndi nkhanza.” Bungwelo linanenanso kuti munthu ali ndi ufulu wofotokoza maganizo ake koma palinso malamulo oletsa kugwiritsa ntchito ufuluwu pofuna kuvutitsa anthu ena. Choncho bungwelo linati “zimene wailesiyo inachita n’zosavomerezeka.”

Bungweli linanenanso kuti nkhani zabodza zimene zinanenedwa zokhudza a Mboniwo zinali zoopsa kwambiri. Linadzudzulanso zimene siteshoni ya TV ya SKAT komanso atolankhani ake anachita pokana kuvomereza kulakwa kwawo. Pofuna kusonyeza anthuwa kuti analakwitsa kwambiri, bungweli linawalamula kuti apereke chindapusa chokwera kwambiri.

Zimene Bungweli Lachita Zithandiza Kuti Chilungamo Chichitike

A Mboni akuyamikira kwambiri bungweli chifukwa chochitapo kanthu pa zimene atolankhani anachita pofalitsa nkhani zokondera komanso zabodza zimene cholinga chake chinali kuipitsa mbiri ya a Mboniwo. Kuonjezera pamenepo, zimenezi zathandiza kuchenjeza anthu enanso amene amafalitsa nkhani ku Bulgaria kuti asamalembenso nkhani zabodza komanso zonyoza a Mboni.

A Krassimir Velev, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Bulgaria ananena kuti: “Palibe amene amafuna kuti anthu ena azifalitsa nkhani zabodza zokhudza iyeyo ndipo ifenso sitifuna kuti anthu azifalitsa nkhani zabodza zokhudza ifeyo. Chifukwa chakuti anthu m’dziko la Bulgaria amva nkhani zabodza zokhudza Mboni za Yehova, mpofunika kuti amve zoona ndipo ndife osangalala kuti bungweli lachitapo kanthu ndi cholinga choti pachitike chilungamo.”

^ ndime 5 Pa 8 July, 2015, siteshoni ya TV ya SKAT inawonetsanso vidiyo yosonyeza nkhanza zimene anthu anachitira a Mboni pa 17 April, 2011. Siteshoniyi inachita zimenezi popitiriza cholinga chake chopangitsa anthu kukhala ndi maganizo olakwika okhudza a Mboni komanso kuti anthu azidana nawo.