Pitani ku nkhani yake

JANUARY 15, 2016
AZERBAIJAN

Azimayi Apitirizabe Kukhala M’ndende Chifukwa Woweruza Anaimitsanso Mlandu Wawo

Azimayi Apitirizabe Kukhala M’ndende Chifukwa Woweruza Anaimitsanso Mlandu Wawo

Pa 14 January 2016, woweruza wa khoti lina la mumzinda wa Baku m’dziko la Azerbaijan, dzina lake Akram Gahramanov, anaimitsanso mlandu wa a Zakharchenko ndi a Jabrayilova. Iye ananena kuti sangapitirize mlanduwu popanda a Zakharchenko, omwe sanathe kupita kukhoti chifukwa choti ankadwala kwambiri. Woweruzayo ananena kuti mlanduwu udzapitirizidwa pa 28 January 2016.

Izi zachititsa kuti maloya a a Zakharchenko ndi a Jabrayilova asakhale ndi mwayi wofotokozera khoti mfundo zothandiza kuti azimayiwa atulutsidwe m’ndendemo. Azimayi awiriwa akudwala chifukwa choti akhala m’ndende kwa miyezi 11. Choncho ngati khotili lingapitirize kuimitsa mlanduwu ndiponso kunena kuti a Zakharchenko ayenera kupezekapo ndiye kuti akuwachitira nkhanza.