Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

JUNE 15, 2015
AZERBAIJAN

A Mboni za Yehova Akufunitsitsa Kuti Boma la Azerbaijan Lisiye Kuwamanga Popanda Mlandu

A Mboni za Yehova Akufunitsitsa Kuti Boma la Azerbaijan Lisiye Kuwamanga Popanda Mlandu

Pa February 17, 2015, apolisi ku Azerbaijan anamanga ndi kusunga azimayi awiri a Mboni za Yehova chifukwa chakuti ankauza ena zimene amakhulupirira. Iwo akhala akusungidwa m’malo amene anthu amakhala poyembekezera kuzengedwa mlandu ndipo akukhala mozunzika kwambiri ngati kuti ndi zigawenga zoopsa. Mvetserani zimene woimira bungwe la Mboni za Yehova za ku Ulaya ananena zokhudza mavuto amene azimayiwa akukumana nawo.